Mika 3 BL92

Cilangizo ca Mulungu cifukwa ca atsogoleri ndi aneneri onyenga

1 Ndipo ndinati, Imvanitu, inu akuru a Yakobo, ndi oweruza a nyumba ya Israyeli; simuyenera kodi kudziwa ciweruzo?

2 inu amene mudana naco cokoma ndi kukondana naco coipa; inu akumyula khungu lao pathupi pao, ndi mnofu wao pa mafupa ao;

3 inu amene mukudyanso mnofu wa anthu anga; ndi kusenda khungu lao ndi kutyola mafupa ao; inde awaduladula ngati nyama yoti aphike, ndi ngati nyama ya mumphika.

4 Pamenepo adzapfuulira kwa Yehova, koma sadzawayankha; inde, adzawabisira nkhope yace nthawi yomweyo, monga momwe anaipsa macitidwe ao.

5 Atero Yehova za aneneriakulakwitsa anthu anga; akuluma ndi mano ao, ndi kupfuula, Mtendere; ndipo, ali yense wosapereka m'kamwa mwao, amkonzera nkhondo;

6 cifukwa cace kudzakhala ngati usiku kwa inu, wopanda masomphenya; ndipo kudzadera inu, wopanda kulosa; ndi dzuwa lidzalowera aneneri, ndi usana udzawadera bii.

7 Ndipo alauli adzacita manyazi, ndi olosa adzathedwa nzeru; ndipo onsewo adzasunama; pakuti kuyankha kwa Mulungu kulibe.

8 Koma ine ndidzala nayo mphamvu mwa Mzimu ya Yehova, ndi ciweruzo, ndi camuna, kufotokozera Yakobo kulakwa kwace, ndi kwa Israyeli cimo lace.

9 Tamvanitu ici, akuru a nyumba ya Yakobo inu, ndi oweruza a nyumba ya Israyeli inu, akuipidwa naco ciweruzo, ndi kupotoza zoongoka zonse.

10 Amanga Ziyoni ndi mwazi, ndi Yerusalemu ndi cisalungamo.

11 Akuru ace aweruza cifukwa ca mphotho, ndi ansembe ace aphunzitsa cifukwa ca malipo, ndi aneneri ace alosa cifukwa ca ndarama; koma atsamira pa Yehova, nati, Kodi Yehova sali pakati pa ife? palibe coipa codzatigwera.

12 Momwemo Ziyoni adzalimidwa ngati: munda cifukwa ca inu, ndi m'Yerusalemu mudzasanduka miunda, ndi phiri la nyumba ngati misanje ya m'nkhalango.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7