6 Cifukwa cace ndidzaika Samariya ngati mulu wa miyala ya m'munda, ngati zooka m'munda wamphesa; ndipo ndidzataya miyala yace m'cigwa, ndi kufukula maziko ace.
7 Ndi mafano ace osema onse adzaphwanyika, ndi mphotho zace zonse zidzatenthedwa ndi moto, ndi mafano ace onse ndidzawapasula; pakuti anazisonkhanitsa pa mphotho ya mkazi waciwerewere, ndipo zidzabwerera ku mphotho ya mkazi waciwerewere.
8 Cifukwa ca ici ndidzacita maliro, ndi kucema, ndidzayenda wolandidwa ndi wamarisece; ndidzalira ngati mimbulu, ndi kubuma ngati nthiwatiwa.
9 Pakuti mabala ace ndi osapola; pakuti afikira ku Yuda; afikira ku cipata ca anthu anga, ku Yerusalemu.
10 Musacifotokoza m'Gati, musalira misozi konse; m'nyumba ya Afira ndinagubuduka m'pfumbi.
11 Pitiratu, wokhala m'Safiri iwe, wamarisece ndi wamanyazi; wokhala m'Zanana sanaturuka; maliro a Betezeli adzakulandani pokhala pace.
12 Pakuti wokhala m'Maroti alindira cokoma, popeza coipa catsika kwa Yehova kumka ku cipata ca Yerusalemu.