7 Kodi adzati, Nyumba ya Yakobo iwe, Mzimu wa Yehova waperewera kodi? izi ndi nchito zace kodi? Mau anga samcitira zokoma kodi, iye amene ayenda coongoka?
8 Koma ngakhale dzulo anthu anga anauka ngati mdani; mukwatula copfunda ku maraya a iwo opitirira mosatekeseka, ngati anthu osafuna nkhondo.
9 Muwataya akazi a anthu anga kunja kwa nyumba zao zokondweretsa; mucotsa ulemerero wanga kwa ana ao kosatha.
10 Nyamukani, cokani, pakuti popumula panu si pano ai; cifukwa ca udio Wakuononga ndi cionongeko cacikuru.
11 Munthu akayenda ndi mtima wacinyengo ndi kunama, ndi kuti, Ndidzanenera kwa iwe za vinyo ndi cakumwa cakuledzeretsa; iye ndiye mneneri wa anthu ace.
12 Ndidzakumemezani ndithu, Yakobo, inu nonse; ndidzasonkhanitsa ndithu otsala a Israyeli; ndidzawaika pamodzi ngati nkhosa za ku Boma; ngati zoweta pakati pa busa pao adzacita phokoso cifukwa ca kucuruka anthu.
13 Wotyola wakwera pamaso pao; iwo anatyola, napita kucipata, naturuka pomwepo; ndi mfumu yao yapita pamaso pao, ndipo Yehova awatsogolera.