1 Koma kudzacitika masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pamwamba pa mapiri, nilidzakuzika pamwamba pa zitunda; ndi mitundu ya anthu idzayendako.
2 Ndipo amitundu ambiri adzamuka, nadzati, Tiyeni, tikwere ku phiri la Yehova, ndi ku nyumba ya Mulungu wa Yakobo; kuti Iye atiphunzitse njira zace, ndipo tidzayenda m'mabande ace; pakuti ku Ziyoni kudzaturuka cilamulo, ndi ku Yerusalemu mau a Yehova.
3 Ndipo Iye adzaweruza mwa mitundu yambiri ya anthu, nadzadzudzula amitundu amphamvu ali kutali; ndipo iwo adzasula malupanga ao akhale makasu, ndi mikondo yao ikhale mazenga, mtundu wa anthu sudzasamulira mtundu unzace lupanga, kapena kuphunziranso nkhondo.
4 Koma adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wace, ndi patsinde pa mkuyu wace; ndipo sipadzakhala wakuwaopsa; pakuti pakamwa pa Yehova wa makamu padanena.
5 Pakuti mitundu yonse ya anthu idzayenda, wonse m'dzina la mlungu wace, ndipo ife tidzayenda m'dzina la Yehova Mulungu wathu ku nthawi yomka muyaya.