9 Tsono upfuulitsa cifukwa ninji? palibe mfumu mwa iwe kodi? watayika kodi mu uphungu wako, kuti zowawa zakugwira ngati mkazi wobala?
10 Imva zowawa, nuyesetse kubala, mwana wamkazi wa Ziyoni, ngati mkazi wakubala; pakuti udzaturuka m'mudzi tsopano, nudzakhala kuthengo, nudzafika ku Babulo; komweko udzapulumutsidwa; komweko Yehova adzakuombola m'manja a adani ako.
11 Ndipo tsopano amitundu ambiri asonkhana kuyambana nawe, akuti, Aipsidwe, diso lathu lipenye ku Ziyoni.
12 Koma sadziwa zolingirira za Yehova, kapena kuzindikira uphungu wace; pakuti anawasonkhanitsa ngati mitolo kudwale.
13 Nyamuka nupunthe, mwana wamkazi wa Ziyoni; pakuti ndidzasanduliza nyanga yako ikhale yacitsulo, ndi ziboda zako zikhale zamkuwa; ndipo udzaphwanya mitundu yambiri ya anthu; ndipo uzipereka ciperekere phindu lao kwa Yehova, ndi cuma cao kwa Ambuye wa dziko lonse lapansi.