1 Tamverani tsono conena Yehova: Nyamuka, tsutsana nao mapiri, ndi zitunda zimve mau ako.
2 Tamvani, mapiri inu, citsutsano ca Yehova, ndi inu maziko olimba a dziko lapansi; pakuti Yehova ali naco citsutsano ndi anthu ace, ndipo adzatsutsana ndi Israyeli.
3 Anthu anga inu, ndakucitirani ciani? ndakulemetsani ndi ciani? citani umboni wonditsutsa.
4 Pakuti ndinakukwezani kukuturutsani m'dziko la Aigupto, ndi kuombola inu m'nyumba ya ukapolo; ndipo ndinatuma akutsogolereni Mose, Aroni, ndi Miriamu.