16 Nati Rute, Musandiumirize kuti ndikusiyeni, ndi kubwerera osakutsatani; pakuti kumene mumukako ndimuka inenso, ndi kumene mugonako ndigona inenso; anthu a kwanu ndiwo anthu a kwa inenso, ndi Mulungu wanu ndiye Mulungu wanga;
17 kumene mudzafera inu ine ndidzafera komweko, ndi kuikidwa komweko; andilange Yehova naonjezeko, ciri conse cikasiyanitsa inu ndi ine, koma imfa ndiyo.
18 Ndipo pakuona kuti analimbika kumuka naye, analeka kulankhula naye.
19 Namuka iwo awiriwo mpaka anafika ku Betelehemu. Ndipo kunali pakufika iwo ku Betelehemu, mudzi wonse unapokosera za iwo; nati, Kodi uyu ndi Naomi?
20 Koma ananena nao, Musandicha Naomi, mundiehe Mara; pakuti Wamphamvuyonse anandicitira zowawa ndithu.
21 Ndinacoka pane wolemera, nandibwezanso kwathu Yehova wopanda kanthu; mundicheranji Naomi, popeza Yehova wandicitira umboni wakunditsutsa, ndi Wamphamvuyonse wandicitira cowawa?
22 Momwemo anabwera Naomi ndi Rute Mmoabu mpongozi wace pamodzi naye, amene anabwera kucokera ku dziko la Moabu; ndipo anafika ku Betelehemu, pakuyamba anthu kuceka barele.