1 Ndipo Naomi anali nave mbale wa mwamuna wace, ndiye munthu mwini cuma cambiri wa banja la Elimeleki; dzina lace ndiye Boazi.
2 Nati Rute Mmoabu kwa Naomi, Mundilole ndimuke kumunda, ndikatole khunkha is ngala za tirigu, kumtsata iye amene adzandikomeramtima. Nanena naye, Muka, mwana wanga.
3 Namuka iye, nakatola khunkha m'munda namatsata ocekawo; ndipo kudangotero naye kuti deralo la munda linali la Boazi, ndiye wa banja la Elimeleki.
4 Ndipo taona, Boazi anafuma ku Betelehemu, nati kwa oceka, Yehova akhale nanu. Namyankha iwo, Yehova akudalitseni.
5 Nati Boazi kwa mnyamata wace woyang'anira ocekawo, Mkazi uyu ngwa yani?
6 Ndipo mnyamata woyang'anira ocekawo anayankha nati, Ndiye mkazi Mmoabuyo anabwera ndi Naomi ku dziko la Moabu;
7 ndipo anati, Undilole, ndikunkhe ndiole pakati pa mitolo potsata ocekawo; nadza iye nakhalakhala kuyambira m'mawa mpaka tsopano; koma m'nyumba samakhalitsamo.
8 Pamenepo Boazi ananena ndi Rute, Ulikumva, mwana wanga? Usakakunkha m'munda mwina, kapena kupitirira pano, koma uumirire adzakazi anga mommuno.
9 Maso ako akhale pa munda acekawo, ndi kuwatsata; kodi sindinawauza anyamata asakukhudze? Ndipo ukamva ludzu, muka kumitsuko, ukamweko otunga anyamatawo,
10 Potero anagwa nkhope yace pansi, nadziweramira pansi, nanena naye, Mwandikomera mtima cifukwa ninji kuti mundisamalira ine, popeza ndine mlendo?
11 Ndipo Boazi anayankha nanena naye, Anandifotokozera bwino zonse unacitira mpongozi wako atafa mwamuna wako; ndi kuti wasiya atate wako ndi mako, ndi dziko lobadwirako iwe, ndi kudza kwa anthu osawadziwa iwe kale.
12 Yehova akubwezere nchito yako, nakupatse mphotho yokwanira Yehova, Mulungu wa Israyeli, amene unadza kuthawira pansi pa mapiko ace.
13 Nati iye, Mundikomere mtima mbuye wanga, popeza mwandisangalatsa, popezanso mwanena cokondweretsa mtima wa mdzakazi wanu, ndingakhale ine sindine ngati mmodzi wa adzakazi anu.
14 Ndipo pa nthawi ya kudya Boazi ananena naye, Sendera kuno, nudyeko mkate; nusunse nthongo yako m'vinyo wosasayo. Nakhala iye m'mbali mwa ocekawo; ndipo anamtambasulira dzanja kumninkha tirigu wokazinga, nadya iye, nakhuta, nasiyapo.
15 Ndipo ataumirira kukatola khunkha, Boazi analamulira anyamata ace ndi kuti, Atole khunkha ngakhale pakati pa mitolo, musamcititse manyazi.
16 Ndiponso mumtayire za m'manja, ndi kuzisiya, natole khunkha, osamdzudzula.
17 Natola khunka iye m'munda mpaka madzulo; naomba khunkhalo napeza ngati licero la barele,
18 nalisenza nalowa kumudzi; ndipo mpongozi wace anaona khunkhalo; Rute naturutsanso nampatsa mkute uja anausiya atakhuta.
19 Ndipo mpongozi wace ananena naye, Unakatola kuti khunkha lero? ndi nchito udaigwira kuti? Adalitsike iye amene anakusamalira. Ndipo anamfotokozera mpongozi wace munthu amene anakagwirako nchito, nati, Dzina lace la munthuyo ndinakagwirako nchito lero ndiye Boazi.
20 Nati Naomi kwa mpongozi wace, Yehova amdalitse amene sanaleka kuwacitira zokoma amoyo, ndi akufa. Ndipo Naomi ananena baye, Munthuyu ndiye mbale wathu, ndiye mmodzi wa iwo otiombolera colowa.
21 Ndipo Rute Mmoabu anati, Ananenanso nane ndithu, Uwaumirire anyamata anga, mpaka atatha kuceka zanga zonse za m'minda.
22 Nati Naomi kwa Rute mpongozi wace, Ncabwino, mwana wanga, kuti uzituruka nao adzakazi ace, ndi kuti asakukomane m'munda wina uti wonse.
23 Momwemo anaumirira adzakazi a Boazi kuti atole khunkha kufikira atatha kuceka barele ndi tirigu; ndipo anakhala iye kwao kwa mpongozi wace.