Rute 4 BL92

Boazi akwatira Rute nabadwa Obedi

1 Ndipo Boazi anakwera kumka kucipata, nakhala pansi pomwepo; ndipo taona, woombolera winayo adanena Boazi analinkupita; nati iye, Iwe uje, pambuka, khala pansi apa; napambuka iye, nakhala pansi.

2 Ndipo anatenga amuna khumi a akulu a mudzi, nati, Mukhale pansi apa. Nakhala pansi iwo.

3 Pamenepo anati kwa woombolerayo, Naomi anabwerayo ku dziko la Moabu ati agulitse kadziko kala kadali ka mbale wathu Elimeleki;

4 ndipo ndati ndikuululira ici, ndi kuti, Ugule aka pamaso pa nzika, ndi pamaso pa akulu a anthu a kwathu. Ukafuna kuombola ombola; koma ukapanda kuombola, undiuze, ndidziwe; pakuti palibe woombola koma iwe, ndi ine pambuyo pako. Pamenepo anati, Ndidzaombola.

5 Nati Boazi, Tsiku lomwelo ugula mundawo pa dzanja la Naomi, uugulanso kwa Rute, Mmoabu, mkazi wa wakufayo, kuukitsira dzina la wakufayo pa colowa cace.

6 Ndipo woombolerayo anati, Sindikhoza kuuombola kwa ine ndekha, ndingaononge colowa canga; udzitengere wekha mphamvu yanga yakuombola; popeza sinditha kuombola.

7 Koma kale m'Israyeli pakuombola ndi pakusinthana, kutsimikiza mlandu wonse, akatero: munthu abvula nsapato yace, naipereka kwa mnansi wace; ndiwo matsimikizidwe m'Israyeli.

8 Ndipo woombolayo anati kwa Boazi, Udzigulire wekha kadzikoko. Nabvula nsapato yace.

9 Nati Boazi kwa akulu, ndi kwa anthu onse, Inu ndinu mboni lero lino kuti ndagula zonse za Elimeleki, ndi zonse za Kilioni, ndi Maloni, pa dzanja la Naomi.

10 Ndiponso Rute Mmoabu, mkazi wa Maloni ndamgula akhale mkazi wanga kuukitsa dzina la wakufayo pa colowa cace; kuti dzina la wakufayo lisaiwalike pakati pa abale ace, ndi pa cipata ca malo ace; inu ndinu mboni lero lino.

11 Pamenepo anthu onse anali kucipata, ndi akuru, anati, Tiri mboni ife. Yehova acite kuti mkazi wakulowayo m'nyumba mwako ange Rakele ndi Leya, amene anamanga nyumba ya Israyeli, iwo awiri; nucite iwe moyenera m'Efrata, numveke m'Betelehemu;

12 ndi nyumba yako inge nyumba ya Perezi, amene Tamare anambalira Yuda, ndi mbeu imene Yehova adzakupatsa ya namwali uyu.

13 Momwemo Boazi anatenga Rute, nakhala iye mkazi wace; ndipo analowa kwa iye; nalola Yehova kuti aime, ndipo anabala mwana wamwamuna.

14 Pamenepo akazi anati kwa Naomi, Adalitsike Yehova amene sana lola kuti akusowe woombolera lero; nilimveke dzina lace m'Israyeli,

15 Nakhale uyu wakukubwezera moyo, ndi wodyetsa ukalamba wako; pakuti mpongozi wako amene akukonda, amene aposa ana amuna asanu ndi awiri kukuthandiza, anambala.

16 Ndipo Naomi anamtenga mwanayo, namuika pacifuwa pace, nakhala mlezi wace.

17 Ndi akazi anansi ace anamucha dzina, ndi kuti, Kwa Naomi kwambadwira mwana; namucha dzina lace Ohedi; ndiye atate wa Jese atate wa Davide.

18 Iyo ndiyo mibadwo ya Perezi; Perezi anabala Hezironi;

19 ndi Hezironi anabala Ramu, ndi Ramu anabala Aminadabu;

20 ndi Aminadabu anabala Nasoni, ndi Nasoni anabala Salimoni;

21 ndi Salimoni anabala Boazi, ndi Boazi anabala Obedi;

22 ndi Obedi anabala Jese, ndi Jese anabala Davide.

Mitu

1 2 3 4