Rute 3 BL92

Boazi anena za kumuombolera Rute colowa

1 Pamenepo Naomi mpongozi wace ananena naye, Mwana wanga, kodi ndisakufunire popumulako, kuti ukhale bwino?

2 Nanga Boazi wodziwana nafe, amene unakhala nao adzakazi ace? Taona, usiku uno apuntha barele popunthirapo.

3 Usambe tsono, nudzole, nubvale zobvala zako, nutsikire popunthirapo, koma usadziwike naye munthuyo, koma atatha kudya ndi kumwa ndiko.

4 Ndipo kudzali, akagona, upenye apo ati agone, numuke, nubvundukule ku mapazi ace, nugone, ndi iyeyo adzakufotokozera zoyenera kucita iwe.

5 Ndipo ananena naye, Zonse muzinena ndidzacita.

6 Pamenepo anatsikira popunthirapo, nacita zonse monga umo mpongozi wace adamuuza.

7 Ndipo atatha Boazi kudya ndi kumwa, nusekerera mtima wace, anakagona kuthungo kwa mulu wa tirigu; nadza iye kacetecete, nabvuodukula ku mapazi ace, nagona.

8 Ndipo kunali, pakati pa usiku munthuyo anadzidzimuka, natembenuka; ndipo taona pa mapazi ace pagona mkazi.

9 Nati iye, Ndiwe yani? Nayankha iye, Ndine Rute mdzakazi wanu; mupfunde mdzakazi wanu copfunda canu, pakuti inu ndinu wondiombolera colowa.

10 Nati iye, Yehova akudalitse, mwana wanga. Cokoma cako wacicita potsiriza pano, ciposa cakuyamba cija, popeza sunatsata anyamata, angakhale osauka angakhale acuma.

11 Ndipo tsopano, mwana wanga, usaope; ndidzakucitira zonse unenazi; pakuti onse a pa mudzi wa anthu a mtundu wanga adziwa kuti iwe ndiwe mkazi waulemu.

12 Tsopano ndipo, zoonadi, ine ndine wakukuombolera colowa, koma pali wakukuombolera woposa ine.

13 Gona usiku uno, ndipo kudzali m'mawa, akakuombolera, cabwino, akuombolere; koma ngati safuna kukuombolera, pali Yehova, ndidzakuombolera colowa ndine; gona mpaka m'mawa.

14 Nagona ku mapazi ace mpaka m'mawa; nalawira asanazindikirane anthu, Pakuti anati, Cisadziwike kuti mkaziyo anadza popunthirapo,

15 Ndipo anati, Bwera naco copfunda cako, nucigwire; nacigwira iye; ndipo anayesa miyeso isanu ndi umodzi ya barele, namsenza; atatero analowa m'mudzi.

16 Ndipo pamene anadza kwa mpongozi wace, iye anati, Wapeza bwanji, mwana wanga? Pamenepo anamfotokozera zonse anamcitira munthuyo.

17 Natinso, Miyeso iyi isanu ndi umodzi ya barele anandipatsa, pakuti anati, Usafike kwa mpongozi wako wopanda kanthu.

18 Ndipo anati, Khala ulipo, mwana wanga; mpaka udziwa umo ukhalire mlandu; pakuti munthuyo sadzauleka mpaka atautha mlanduwo lero lino.

Mitu

1 2 3 4