3 Namuka iye, nakatola khunkha m'munda namatsata ocekawo; ndipo kudangotero naye kuti deralo la munda linali la Boazi, ndiye wa banja la Elimeleki.
4 Ndipo taona, Boazi anafuma ku Betelehemu, nati kwa oceka, Yehova akhale nanu. Namyankha iwo, Yehova akudalitseni.
5 Nati Boazi kwa mnyamata wace woyang'anira ocekawo, Mkazi uyu ngwa yani?
6 Ndipo mnyamata woyang'anira ocekawo anayankha nati, Ndiye mkazi Mmoabuyo anabwera ndi Naomi ku dziko la Moabu;
7 ndipo anati, Undilole, ndikunkhe ndiole pakati pa mitolo potsata ocekawo; nadza iye nakhalakhala kuyambira m'mawa mpaka tsopano; koma m'nyumba samakhalitsamo.
8 Pamenepo Boazi ananena ndi Rute, Ulikumva, mwana wanga? Usakakunkha m'munda mwina, kapena kupitirira pano, koma uumirire adzakazi anga mommuno.
9 Maso ako akhale pa munda acekawo, ndi kuwatsata; kodi sindinawauza anyamata asakukhudze? Ndipo ukamva ludzu, muka kumitsuko, ukamweko otunga anyamatawo,