3 Usambe tsono, nudzole, nubvale zobvala zako, nutsikire popunthirapo, koma usadziwike naye munthuyo, koma atatha kudya ndi kumwa ndiko.
4 Ndipo kudzali, akagona, upenye apo ati agone, numuke, nubvundukule ku mapazi ace, nugone, ndi iyeyo adzakufotokozera zoyenera kucita iwe.
5 Ndipo ananena naye, Zonse muzinena ndidzacita.
6 Pamenepo anatsikira popunthirapo, nacita zonse monga umo mpongozi wace adamuuza.
7 Ndipo atatha Boazi kudya ndi kumwa, nusekerera mtima wace, anakagona kuthungo kwa mulu wa tirigu; nadza iye kacetecete, nabvuodukula ku mapazi ace, nagona.
8 Ndipo kunali, pakati pa usiku munthuyo anadzidzimuka, natembenuka; ndipo taona pa mapazi ace pagona mkazi.
9 Nati iye, Ndiwe yani? Nayankha iye, Ndine Rute mdzakazi wanu; mupfunde mdzakazi wanu copfunda canu, pakuti inu ndinu wondiombolera colowa.