1 Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yona nthawi yaciwiri, ndi kuti,
2 Nyamuka, pita ku Nineve mudzi waukuru uja, nuulalikire uthenga umene ndikuuza.
3 Ndipo Yona ananyamuka, napita ku Nineve, monga mwa mau a Yehova. Koma Nineve ndiwo mudzi waukuru pamaso pa Yehova, wa ulendo wa masiku atatu.
4 Ndipo Yona anayamba kulowa mudziwo ulendo wa tsiku limodzi, nalalikira, nati, Atsala masiku makumi anai ndipo Nineve adzapasuka.
5 Ndipo anthu a Nineve anakhulupirira Mulungu, nalalikira cosala, nabvala ciguduli, kuyambira wamkuru kufikira wamng'ono wa iwowa.