5 Galamukani, oledzera inu, nimulire; bumani, nonse akumwa vinyo, cifukwa ca vinyo watsopano; pakuti waletsedwa pakamwa panu.
6 Pakuti mtundu wadza, wakwerera dziko langa, wamphamvu wosawerengeka, mano ace akunga mano a mkango, nukhala nao mano acibwano a mkango waukuru.
7 Unaonongadi mpesa wanga, nunyenya mkuyu wanga, nuukungudza konse, nuutaya; nthambi zace zasanduka zotumbuluka.
8 Lirani ngati namwali wodzimangira m'cuuno ciguduli, cifukwa ca mwamuna wa unamwali wace.
9 Nsembe yaufa ndi nsembe yothira zalekeka ku nyumba ya Yehova; ansembe, atumiki a Yehova, acita maliro.
10 M'munda mwaonongeka, nthaka ilira; pakuti tirigu waonongeka, vinyo watsopano wamwelera, mafuta akudza pang'onong'ono.
11 Gomani, akulima m'minda inu; lirani, akulima mpesa; cifukwa ca tirigu ndi barele; pakuti dzinthu za m'minda zatayika.