1 MAU a Yehova a kwa Yoeli mwana wa Petueli.
2 Imvani ici, akulu akulu inu, nimuchere khutu, inu nonse okhala m'dziko. Cacitika ici masiku anu kodi, kapena masiku a makolo anu?
3 Mufotokozere ana anu ici, ndi ana anu afotokozere ana ao, ndi ana ao afotokozere mbadwo wina.
4 Cosiya cimbalanga, dzombe lidacidya; ndi cosiya dzombe, cirimamine adacidya; ndi cosiya cirimamine, anoni adacidya.
5 Galamukani, oledzera inu, nimulire; bumani, nonse akumwa vinyo, cifukwa ca vinyo watsopano; pakuti waletsedwa pakamwa panu.
6 Pakuti mtundu wadza, wakwerera dziko langa, wamphamvu wosawerengeka, mano ace akunga mano a mkango, nukhala nao mano acibwano a mkango waukuru.
7 Unaonongadi mpesa wanga, nunyenya mkuyu wanga, nuukungudza konse, nuutaya; nthambi zace zasanduka zotumbuluka.
8 Lirani ngati namwali wodzimangira m'cuuno ciguduli, cifukwa ca mwamuna wa unamwali wace.
9 Nsembe yaufa ndi nsembe yothira zalekeka ku nyumba ya Yehova; ansembe, atumiki a Yehova, acita maliro.
10 M'munda mwaonongeka, nthaka ilira; pakuti tirigu waonongeka, vinyo watsopano wamwelera, mafuta akudza pang'onong'ono.
11 Gomani, akulima m'minda inu; lirani, akulima mpesa; cifukwa ca tirigu ndi barele; pakuti dzinthu za m'minda zatayika.
12 Mpesa wauma, mkuyu wafota, mtengo wa mkangaza ndi kanjedza ndi muula, inde mitengo yonse ya kuthengo yafota; pakuti cimwemwe cathera ana a anthu.
13 Mudzimangire ciguduli m'cuuno mwanu, nimulire ansembe inu; bwnani, otumikira ku guwa la nsembe inu; lowani, gonani usiku wonse m'ciguduli, inu otumikira Mulungu wanga; pakuti nsembe yaufa ndi nsembe yothira zaletsedwera nyumba ya Mulungu wanu.
14 Patulani tsiku losala, lalikirani masonkhano oletsa, sonkhanitsani akulu akulu, ndi onse okhala m'dziko, ku nyumba ya Yehova Mulungu wanu; nimupfuulire kwa Yehova.
15 Kalanga ine, tsikuli! pakuti layandikira tsiku la Yehova, lidzafika ngati cionongeko cocokera kwa Wamphamvuyonse.
16 Cakudya sicicotsedwa kodi pamaso pathu? cimwemwe ndi cikondwerero pa nyumba ya Mulungu wathu?
17 Mbeu zaola pansi pa zibuluma zao; zosungiramo zaonongeka, nkhokwe zapasuka; pakuti tirigu wakwinyata.
18 Ha! nyama ziusa moyo, magulu a ng'ombe azimidwa; pakuti zisowa podyera; magulu a nkhosa omwe atha.
19 Ndipfuulira kwa Inu Yehova, pakuti moto wapsereza mabusa a m'cipululu, ndi malawi a moto anatentha mitengo yonse ya kuthengo,
20 inde nyama za kuthengo zilira kwa Inu; pakuti mitsinje yamadzi yaphwa, ndi moto wapsereza mabusa a m'cipululu.