Yoweli 3 BL92

Aneneratu za cilango ca Mulungu pa adani ace; Israyeli adzakonrekanso

1 Pakuti taonani, masiku awo, ndi nthawi iyo, pamene ndibwera nao andende a Yuda ndi a Yerusalemu,

2 ndidzasonkhanitsa amitundu onse, ndi kutsikira nao ku cigwa ca Yosafati; ndipo ndidzaweruzana nao komweko za anthu anga, ndi colowa canga Israyeli, amene anawabalalitsa mwa amitundu, nagawa dziko langa,

3 Ndipo anacitira anthu anga maere, napereka mwana wamwamuna kusinthana ndi mkazi wadama, nagula vinyo ndi mwana wamkazi kuti amwe.

4 Ndiponso ndiri ndi ciani ndi inu, Turo ndi Zidoni, ndi malire onse a Afilisti? mudzandibwezera cilango kodi? Mukandibwezera cilango msanga, mofulumira, ndidzabwezera cilango canu pamutu panu,

5 Popeza inu munatenga siliva wanga ndi golidi wanga, ndi kulonga zofunika zanga zokoma m'akacisi anu;

6 munagulitsanso ana a Yuda ndi ana a Yerusalemu kwa ana a Yavani, kuwacotsa kutali kwa malire ao;

7 taonani, ndidzawautsa kumalo kumene munawagulitsako, ndi kubwezera cilango canu pamutu panu;

8 ndipo ndidzagulitsa ana ako amuna ndi akazi m'dzanja la ana a Yuda; ndipo iwo adzawagulitsa kwa anthu a Seba, kwa anthu okhala kutari; pakuti Yehova wanena.

9 Mulalikire ici mwa amitundu mukonzeretu nkhondo; utsani amuna amphamvu; amuna onse a nkhondo ayandikire nakwere.

10 Sulani makasu anu akhale malupanga, ndi anangwape anu akhale nthungo; wofoka anene, Ndine wamphamvu.

11 Fulumirani, idzani, amitundu inu nonse pozungulirapo; sonkhanani pamodzi, mutsitsire komweko amphamvu anu, Yehova.

12 Agalamuke amitundu, nakwerere ku cigwa ca Yosafati; pakuti ndidzakhala komweko kuweruza amitundu onse ozungulira,

13 Longani zenga, pakuti dzinthu dzaca; idzani, pondani, pakuti cadzala coponderamo mphesa; zosungiramo zisefuka; pakuti zoipa zao nzazikuru.

14 Aunyinji, aunyinji m'cigwa cotsirizira mlandu! pakuti layandikira tsiku la Yehova m'cigwacotsiriziramlandu.

15 Dzuwa ndi mwezi zada, ndi nyenyezi zibweza kuwala kwao.

16 Ndipo Yehova adzadzuma ali ku Ziyoni, ndi kumveketsa mau ace ali ku Yerusalemu; ndi thambo ndi dziko lapansi zidzagwedezeka; koma Yehova adzakhala copulumukirako anthu ace, ndi linga la ana a Israyeli.

17 Momwemo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu wakukhala m'Ziyoni, phiri langa lopatulika; pamenepo Yerusalemu adzakhala wopatulika, osapitanso alendo pakati pace,

18 Ndipo kudzacitika tsiku ilo mapiri adzakhetsa vinyo wozuna, ndi pazitunda padzayenda mkaka, ndi m'mitsinje yonse ya Yuda mudzayenda madzi; ndi madzi a kasupe adzaturuka m'nyumba ya Yehova, nadzamwetsa madzi cigwa ca Sitimu.

19 Aigupto adzasanduka bwinja, ndi Edomu adzasanduka cipululu copanda kanthu, cifukwa ca ciwawaci anawacitira ana a Yuda; popeza anakhetsa mwazi wosacimwa m'dziko lao.

20 Koma Yuda adzakhala cikhalire, ndi Yerusalemu ku mibadwo mibadwo.

21 Ndipo ndidzayeretsa mwazi wao umene sindinauyeretsa, pakuti Yehova akhala m'Ziyoni.

Mitu

1 2 3