Amosi 1 BL92

Cilango ca Mulungu pa amitundu ozinga Israyeli

1 MAU a Amosi, amene anali mwa oweta ng'ombe a ku Tekoa, ndiwo amene anawaona za Israyeli masiku a Uziya mfumu ya Yuda, ndi masiku a Yerobiamu mwana wa Yoasi mfumu ya Israyeli, zitatsala zaka ziwiri cisanafike cibvomezi.

2 Ndipo anati, Yehova adzadzuma ali m'Ziyoni, nadzamveketsa mau ace ali m'Yerusalemu; podyetsa abusa padzacita cisoni, ndi mutu wa Karimeli udzauma.

3 Atero Yehova, Cifukwa ca zolakwa zitatu za Damasiko, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwace; popeza anapuntha Gileadi ndi zopunthira zacitsulo;

4 koma ndidzatumiza moto ku nyumba ya Hazaeli, ndipo udzanyeketsa nyumba zacifumu za Benihadadi.

5 Ndipo ndidzatyola mpiringidzo wa Damasiko, ndi kulikha okhala m'cigwa ca Aveni, ndi iye wogwira ndodo yacifumu m'Betedeni; ndi anthu a Aramu adzalowa ndende ku Kiri, ati Yehova.

6 Atero Yehova, Cifukwa ca zolakwa zitatu za Gaza, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwace; popeza anatenga ndende anthu onse kuwapereka kwa Edomu;

7 koma ndidzatumiza moto pa linga la Gaza, ndipo udzatha nyumba zace zacifumu;

8 ndipo ndidzalikha okhala m'Asidodi, ndi iye wogwira ndodo yacifumu m'Asikeloni; ndipo ndidzabwezera Ekroni dzanja langa limlange; ndi Afilisti otsala adzatayika, ati Ambuye Yehova.

9 Atero Yehova, Cifukwa ca zolakwa zitatu za Turo, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwace; popeza anapereka anthu onse kwa Edomu, osakumbukila pangano lacibale;

10 koma ndidzatumiza moto pa linga la Turo, ndipo udzanyeketsa nyumba zace zacifumu.

11 Atero Yehova, Cifukwa ca zolakwa zitatu za Edomu, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwace; popeza analondola mphwace ndi lupanga, nafetsa cifundo cace conse, ndi mkwiyo wace unang'amba cing'ambire, nasunga mkwiyo wace cisungire;

12 koma ndidzatumiza moto pa Temani, udzanyeketsa nyumba zacifumu za Bozira.

13 Atero Yehova, Cifukwa ca zolakwa zitatu za ana a Amoni, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwace; popeza anatumbula akazi ali m'pakati a Gileadi, kuti akuze malire ao;

14 koma ndidzayatsa moto pa linga la Raba, udzanyeketsa nyumba zacifumu zace, ndi kupfuula tsiku la nkhondo, ndi namondwe, tsiku la kabvumvulu;

15 ndipo mfumu yao idzalowa kundende, iyo ndi akalonga ace pamodzi, ati Yehova.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9