Amosi 9 BL92

Masomphenya a kulangidwa koopsa. Lonjezo kuti madalitso adzabwera

1 Ndinaona Ambuye alikuima pa guwa la nsembe, nati Iye, Kantha mitu ya nsanamira, kuti ziundo zigwedezeke; nuphwanye mitu yao yonse; ndipo ndidzapha otsiriza ao ndi lupanga; wothawayo mwa iwo sadzathawadi, ndi wopulumukayo mwaiwosadzapulumukadi.

2 Angakhale akumba mpaka kunsi kwa manda, dzanja langa lidzawatenga kumeneko; angakhale akwera kumwamba, ndidzawatsitsa komweko.

3 Angakhale abisala pamwamba pa Karimeli, ndidzawapwaira ndi kuwatenga komweko; angakhale abisala pamaso panga pansi pa nyanja, kumeneko ndidzalamulira njoka, ndipo idzawaluma.

4 Angakhale alowa ndende pamaso pa adani ao, kumeneko ndidzalamulira lupanga, ndipo lidzawapha; ndipo ndidzayang'anitsa maso anga kwa iwowa, kuwacitira coipa, si cokoma ai.

5 Pakuti Ambuye Yehova wa makamu ndiye amene akhudza dziko, nilisungunuka; ndi onse okhalamo adzacita maliro; ndipo lidzakwera lonseli ngati madzi a m'nyanja; nilidzatsikanso ngati nyanja ya m'Aigupto;

6 ndiye amene amanga zipinda zace zosanja m'mwamba, nakhazika tsindwi lace pa dziko lapansi; Iye amene aitana madzi a m'nyanja, nawatsanulira padziko; dzina lace ndiye Yehova.

7 Kodi simukhala kwa Ine ngati ana a Kusi, inu ana a Israyeli? ati Yehova. Sindinakweza Israyeli ndine, kumturutsa m'dziko la Aigupto, ndi Afilisti ku Kafitori, ndi Aaramu ku Kiri?

8 Taonani, maso a Ambuye Yehova ali pa ufumu wocimwawo, ndipo ndidzauononga kuucotsa pa dziko lapansi; pokhapo sindidzaononga nyumba ya Yakobo kuitha konse, ati Yehova.

9 Pakuti taonani, ndidzalamulira, ndipo ndidzapeta nyumba ya Israyeli mwa amitundu onse, monga apeta tirigu m'licero; koma silidzagwa pansi diso, ndi limodzi lonse.

10 Ocimwa onse a anthu anga adzafa ndi lupanga, ndiwo amene akuti, Coipa sicidzatipeza, kapena kutidulira.

11 Tsiku lomwelo ndidzautsa msasa wa Davide udagwawo, ndi kukonzanso zopasuka zace; ndipo ndidzautsa zogumuka zace, ndi kuumanga monga masiku a kalelo;

12 kuti alandire otsala a Edomu akhale colowa cao, ndi amitundu onse akuchedwa dzina langa, ati Yehova wakucita izi.

13 Taonani akudza masiku, ati Yehova, akud wolima adzapezana ndi wodula, ndi woponda mphesa adzapezana ndi wofesa, ndi mapiri adzakhetsa vinyo watsopano, ndi zitunda zonse zidzasungunuka.

14 Ndipo ndidzabwezanso undende wa anthu anga Israyeli, ndipo adzamanganso mabwinja, ndi kukhala m'menemo; nadzaoka minda ya mipesa nadzamwa vinyo wace, nadzalima minda ndi kudya zipatso zace.

15 Ndipo ndidzawaoka m'dziko mwao ndipo sadzazulidwanso m'dziko lao limene ndawapatsa, ati Yehova Mulungu wako.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9