Obadiya 1 BL92

Zoipa zao ndi kulangidwa kwa Aedomu. Dalo la Israyeli

1 MASOMPHENYA a Obadiya. Atero Ambuye Yehova za Edomu: Tamva mbiri yocokera kwa Yehova, ndi mthenga wotumidwa mwa amitundu, ndi kuti, Nyamukani, timuukire kumthira nkhondo.

2 Taona, ndakuika wamng'ono mwa amitundu; unyozedwa kwambiri.

3 Kudzikuza kwa mtima wako kwakunyenga, iwe wokhala m'mapanga a thanthwe, iwe pokhala pako pamwamba, wakunena m'mtima mwace, Adzanditsitsira pansi ndani?

4 Cinkana ukwera pamwamba peni peni ngati ciombankhanga, cinkana cisanja cako cisanjika pakati pa nyenyezi, ndidzakutsitsa kumeneko, ati Yehova.

5 Akakudzera akuba, kapena mbala usiku, (Ha! waonongeka) sadzaba mpaka adzakhuta kodi? Akakudzera akuchera mphesa sadzasiya khunkha kodi?

6 Ha! za Esau zasanthulidwa; ha! zobisika zace zafunidwa.

7 Anthu onse a akupangana nawe anakuperekeza mpaka pamalire; anthu okhala ndi mtendere nawe anakunyenga, nakuposa mphamvu; iwo akudya cakudya cako akuchera msampha pansi pako; mulibe nzeru mwa iye.

8 Ati Yehova, Kodi sindidzaononga tsiku lija anzeru mwa Edomu, ndi luntha m'phiri la Esau?

9 Ndipo amuna anu amphamvu adzatenga nkhawa, Temani iwe, kuti onse aonongeke m'phiri la Edomu, ndi kuphedwa.

10 Cifukwa ca ciwawa unamcitira mphwako Yakobo, udzakutidwa ndi manyazi, nudzaonongeka ku nthawi yonse.

11 Tsiku lija unaima padera, tsiku lija alendo anagwira ndende makamu ace, nalowa m'zipata zace acilendo, nacitira Yerusalemu maere, iwenso unakhala ngati mmodzi wa iwowa.

12 Koma usapenyerera tsiku la mphwako, tsiku loyesedwa mlendo iye, nusasekerere ana a Yuda tsiku la kuonongeka kwao, kapena kuseka cikhakha tsiku lakupsinjika.

13 Usalowe m'mudzi wa anthu anga tsiku la tsoka lao, kapena kupenyerera iwe coipa cao tsiku la tsoka lao, kapena kuthira manja khamu lao tsiku la tsoka lao.

14 Ndipo usaime pamphambano kuononga opulumuka ace; kapena kupereka otsala ace tsiku lakupsinjika.

15 Pakuti tsiku la Yehova layandikira amitundu onse; monga unacita iwe, momwemo adzakucitira; cocita iwe cidzakubwererapamtupako.

16 Pakuti monga munamwa pa phiri langa lopatulika, momwemo amitundu onse adzamwa kosalekeza; inde adzamwa, nadzameza, nadzakhala monga ngati sanalipo.

17 Koma m'phiri la Ziyoni mudzakhala opulumuka, ndipo lidzakhala lopatulika; ndi a nyumba ya Yakobo adzakhala nazo zolowa zao.

18 Ndipo nyumba ya Yakobo idzakhala moto, ndi nyumba ya Yosefe lawi, ndi nyumba ya Esau ngati ciputu, ndipo adzawatentha pakati pao, ndi kuwapsereza; ndipo sadzakhalapo otsalira nyumba ya Esau; pakuti Yehova wanena.

19 Ndipo akumwela adzakhala nalo phiri la Esau colowa cao; ndi iwo a kucidikha adzakhala nalo dziko la Afilisti; ndipo adzakhala nayo minda ya Efraimu, ndi minda ya Samariya colowa cao; ndi Benjamini adzakhala nalo la Gileadi.

20 Ndipo andende a khamu ili la ana a Israyeli, okhala mwa Akanani, adzakhala naco colowa cao mpaka pa Zarefati; ndi andende a ku Yerusalemu okhala m'Sefaradi adzakhala nayo midzi ya kumwela, colowa cao.

21 Ndipo apulumutsi adzakwera pa phiri la Ziyoni kuweruza phiri la Esau; ndipo ufumu udzakhala wace wa Yehova.

Mitu

1