Amosi 5 BL92

Nyimbo ya maliro yakunena za kutyoka kwa Israyeli

1 Tamverani mau awa ndinenawa, akhalire inu nyimbo ya maliro, nyumba ya Israyeli inu.

2 Namwali wa Israyeli wagwa, sadzaukanso; wagwetsedwa pa nthaka yace, palibe womuutsa.

3 Pakuti atero Ambuye Yehova, M'nyumba ya Israyeli, mudzi woturukamo cikwi cimodzi adzautsalira zana limodzi, ndi uwu woturukamo zana limodzi adzautsalira khumi.

4 Pakuti atero Yehova kwa nyumba ya Israyeli, Mundifunefune Ine, ndipo mudzakhala ndi moyo;

5 koma musamafuna Beteli, kapena kumalowa m'Giligala; musamapita ku Beereseba; pakuti Giligala adzalowadi m'ndende, ndi Beteli adzasanduka cabe.

6 Funani Yehova, ndipo mudzakhala ndi mayo; angabuke ngati moto m'nyumba ya Yosefe, ndipo unganyeke wopanda wakuzima m'Beteli;

7 inu osintha ciweruzo cikhale civumulo, nimugwetsa pansi cilungamo,

8 Iye wakulenga Nsangwe ndi Akamwiniatsatana, nasanduliza mdima wandiweyani ukhale m'mawa, nasanduliza usana ude ngati usiku, wakuitana madzi a m'nyanja, nawatsanulira pa dziko lapansi, dzina lace ndiye Yehova;

9 wakufikitsa cionongeko pa wamphamvu modzidzimuka, cionongeko nicigwera linga,

10 Iwo adana naye wodzudzula kucipata, nanyansidwa naye wolunjikitsa mau.

11 Popeza tsono mupondereza aumphawi, ndi kumsonkhetsa tirigu; mwamanga nyumba za miyala yosema, koma simudzakhala m'mwemo; mwaoka minda ya mipesa yokonda, koma simudzamwa vinyo wace.

12 Pakuti ndidziwa kuti zolakwa zanu nzocuruka, ndi macimo anu ndi olimba, inu akusautsa olungama, akulandira cokometsera mlandu, akukankha osowa kucipata.

13 Cifukwa cace wocenierayo akhala cete nthawi yomweyo; pakuti ndiyo nthawi yoipa.

14 Funani cokoma, si coipa ai; kuti mukhale ndi moyo; motero Yehova Mulungu wamakamu adzakhala ndi inu, monga munena.

15 Danani naco coipa, nimukonde cokoma; nimukhazikitse ciweruzo kucipata; kapena Yehova Mulungu wa makamu adzacitira cifundo otsala a Yosefe.

16 Cifukwa cace atero Yehova, Mulungu wa makamu, Ambuye, M'makwalala onse mudzakhala kulira, ndi m'miseu yonse adzati, Kalanga ine! kalanga ine! nadzaitana wakumunda adze kumaliro, ndi odziwa maliridwe a nthetemya alire.

17 Ndi m'minda yonse yamipesa mudzakhala kulira, pakuti ndipita pakati pako, ati Yehova.

18 Tsoka inu akufuna tsiku la Yehova! mudzapindulanji nalo tsiku la Yehova? ndilo mdima, si kuunika ai.

19 Kudzakhala monga munthu akathawa mkango, ndi cimbalangondo cikomana naye; kapena akalowa m'nyumba, natsamira kukhoma ndi dzanja lace, nimluma njoka.

20 Kodi tsiku la Yehova silidzakhala la mdima, si la kuunika ai? lakuda bii, lopanda kuwala m'menemo?

21 Ndidana nao, ndinyoza madyerero anu, sindidzakondwera nao masonkhano anu oletsa.

22 Inde, mungakhale mupereka kwa Ine nsembe zanu zopsereza, ndi nsembe zaufa, sindidzazilandira Ine; ndinsembe zoyamika za ng'ombe zanu zonenepa, sindidzazisamalira Ine.

23 Mundicotsere phokoso la nyimbo zanu; sindifuna kumva mayimbidwe a zisakasa zanu.

24 Koma ciweruzo ciyende ngati madzi, ndi cilungamo ngati mtsinje wosefuka.

25 Ngati munabwera nazo kwa Ine nsembe zophera ndi zaufa zaka makumi anai m'cipululu, inu nyumba ya Israyeli?

26 Inde mwasenza hema wa mfumu yanu, ndi tsinde la mafano anu, nyenyezi ya mlungu wanu, amene mudadzipangira.

27 M'mwemo ndidzakutengani kumka nanu kundende kutsogolo kwa Damasiko, ati Yehova, amene dzina lace ndiye Mulungu wa makamu.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9