1 Tamverani mau awa akunenerani Yehova motsutsa, inu ana a Israyeli, kulinenera banja lonse ndinalikweza kuliturutsa m'dziko la Aigupto, ndi kuti,
2 Inu nokha ndinakudziwani mwa mabanja onse a pa dziko lapansi, m'mwemo ndidzakulangani cifukwa ca mphulupulu zanu zonse.
3 Kodi awiri adzayenda pamodzi asanapanganiranetu?
4 Kodi mkango udzabangula m'nkhalango wosakhala nayo nyama? Kodi msona wa mkango udzalira m'ngaka mwace usanagwire kanthu?
5 Kodi mbalame idzakodwa mumsampha pansi popanda msampha woichera? Kodi msampha ufamphuka pansi wosakola kanthu?
6 Kodi adzaomba lipenga m'mudzi osanieniemera anthu? Kodi coipa cidzagwera mudzi osacicita Yehova?
7 Pakuti Ambuye Yehova sadzacita kanthu osaulula cinsinsi cace kwa atumiki ace aneneri.
8 Mkango ukabangula, ndani amene saopa? Ambuye Yehova wanena, ndani amene sanenera?
9 Bukitsani ku nyumba zacifumu za Asidodi, ndi ku nyumba zacifumu za m'dziko la Aigupto, nimuziti, Sonkhanani pa mapiri a Samariya, ndipo penyani masokosero akuru m'menemo, ndi ozunzika m'kati mwace.
10 Pakuti sadziwa kucita zolungama, amene akundika zaciwawa ndi umbala m'nyumba zao zacifumu, ati Yehova.
11 Cifukwa cace, atero Ambuye Yehova, Padzakhala mdani pozungulira pace pa dziko, nadzatsitsa kukucotsera mphamvu yako; ndi za m'nyumba zako zacifumu adzazifunkha.
12 Atero Yehova, Monga mbusa alanditsa m'kamwa mwa mkango miyendo iwiri, kapena kansonga ka khutu, momwemo adzalanditsidwa ana a Israyeli okhala pansi m'Samariya, m'ngondya ya guwa logonapo, ndi pa mitsamiro ya kama.
13 Tamverani inu, mucitire umboni wotsutsa nyumba ya Yakobo, ati Ambuye Yehova Mulungu wa makamu.
14 Pakuti tsiku lakumlanga Israyeli cifukwa ca zolakwa zace, ndidzalanganso maguwa a nsembe a ku Beteli; ndi nyanga za guwa la nsembe zidzadulidwa, nizidzagwa pansi.
15 Ndipo ndidzakantha nyumba ya nyengo yacisanu, pamodzi ndi nyumba ya nyengo yadzuwa; ndi nyumba zaminyanga zidzaonongeka; ndi nyumba zazikuruzo zidzatha, ati Yehova.