Amosi 2 BL92

1 Atero Yehova, Cifukwa ca zolakwa zitatu za Moabu, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwace; popeza anatentha mafupa a mfumu ya ku Edomu asanduke njereza;

2 koma ndidzatumiza moto pa Moabu, udzanyeketsa nyumba zacifumu za Kerioti; ndipo Moabu adzafa ndi phokoso, ndi kupfuula, ndi mau a lipenga;

3 ndipo ndidzalikha woweruza pakati pace, ndi kupha akalonga ace onse, ati Yehova.

Cilango ca Mulungu pa Yuda ndi Israyeli

4 Atero Yehova, Cifukwa ca zolakwa zitatu za Yuda, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwace; popeza akaniza cilamulo ca Yehova, osasunga malemba ace; ndipo awalakwitsa mabodza ao amene makolo ao anawatsata;

5 koma ndidzatumiza moto pa Yuda, udzanyeketsa nyumba zacifumu za m'Yerusalemu.

6 Atero Yehova, Cifukwa ca zolakwa zitatu za Israyeli, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwace; popeza agulitsa wolungama ndi ndalama, ndi wosowa cifukwa ca nsapato;

7 ndiwo amene aliralira pfumbi lapansi liri pamutu pa wosauka, napotoza njira ya wofatsa; ndipo munthu ndi atate wace amuka kwa namwali yemweyo, kuti aipse dzina langa loyera;

8 nagona pansi pa zopfunda za cikole ku maguwa a nsembe ali onse, ndi m'nyumba ya Mulungu wao akumwa vinyo wa iwo olipitsidwa.

9 Koma ndinaononga Ine pamaso pa Aamori, amene msinkhu wao unanga msinkhu wa mikungudza, nakhala nayo mphamvu ngati thundu; koma ndinaononga zipatso zao m'mwamba, ndi mizu yao pansi.

10 Ndipo ndinakukwezani kucokera m'dziko la Aigupto, ndi kukutsogolerani zaka makumi anai m'cipululu, kuti mulandire dziko la Aamori likhale colowa canu.

11 Ndipo ndinaukitsa mwa ana anu aneneri, ndi mwa anyamata anu Anaziri. Si momwemo, inu ana a Israyeli, ati Yehova?

12 Koma munamwetsa Anaziri vinyo, ndi kulamulira aneneri ndi kuti, Musamanenera.

13 Taonani, ndidzakupsinjani m'malo mwanu, monga lipsinja gareta lodzala ndi mitolo fwa.

14 Ndipo populumukirapo padzasowera waliwiro, ndi wamphamvu; sadzalimbikitsa mphamvu yace, ndi ngwazi siidzapulumutsa moyo wace;

15 ndi wokoka uta sadzalimbika, ndi waliwiro sadzadzipulumutsa; ngakhale woyenda pa akavalo sadzapulumutsa moyo wace;

16 ndi wolimba mtima mwa ngwazi adzathawa wamarisece tsiku lomwelo, ati Yehova.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9