Amosi 8 BL92

Masomphenya a mtanga wa zipatso, Zoopsa za pa Israyeli

1 Ambuye Yehova anandionetsa cotere; ndipo taonani, mtanga wa zipatso zamalimwe.

2 Ndipo anati, Amosi uona ciani? Ndipo ndinati, Mtanga wa zipatso zamalimwe. Nati Yehova kwa ine, Citsiriziro cafikira anthu anga Israyeli, sindidzawalekanso.

3 Koma nyimbo za kukacisi zidzasanduka kubuma tsiku ilo, ati Ambuye Yehova; mitembo idzacuruka; adzaitaya pali ponse padzakhala zii.

4 Tamverani ici, inu akumeza aumphawi, ndi kuwatha ofatsa m'dziko, ndi kuti,

5 Mwezi wokhala upita liti, kuti tigulitse dzinthu? ndi Sabata, kuti titsegulire tirigu? ndi kucepsa efa, ndi kukuliitsa sekeli, ndi kucenjerera nayo miyeso yonyenga;

6 kuti tigule osauka ndi ndarama, ndi aumphawi ndi nsapato, ndi kugulitsa nsadwa za tirigu.

7 Yehova walumbira pali kudzikuza kwa Yakobo, Ngati ndidzaiwala konse nchito zao ziri zonse?

8 Kodi dziko silidzanjenjemera cifukwa ca ici, ndi kulira ali yense wokhalamo? inde lidzakwera lonseli ngati madzi a m'mtsinje; lidzagwedezeka, ndi kutsikanso ngati mtsinje wa Aigupto,

9 Ndipo kudzacitika tsiku lomwelo, ati Ambuye Yehova, ndidzalowetsa dzuwa usana, ndi kudetsa dziko pausana poyera.

10 Ndipo ndidzasanduliza madyerero anu, akhale maliro, ndi nyimbo zanu zikhale za maliro, ndi kufikitsa ziguduli m'cuuno monse, ndi mpala pa mutu uli wonse; nadzakhala ngati maliro a mwana mmodzi yekha, ndi citsiriziro cace ngati tsiku lowawa.

11 Taonani, akudza masiku, ati Ambuye Yehova, akuti ndidzatumiza njala m'dzikomo, si njala ya mkate kapena ludzu la madzi, koma njala ya kumva mau a Yehova.

12 Ndipo adzayendayenda peyupeyu kuyambira kunyanja kufikira kunyanja ndi kuyambira kumpoto kufikira kum'mawa; adzathamangathamanga kufunafuna mau a Yehova, koma osawapeza.

13 Tsiku lomwelo anamwali okongola ndi anyamata adzakomoka nalo ludzu.

14 Iwo akulumbira ndi kuchula cimo la Samariya, ndi kuti, Pali Mulungu wako, Dani; ndipo, Pali moyo wa njira ya ku Beereseba, iwowa adzagwa, osaukanso konse.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9