Amosi 7 BL92

Masomphenya atatu, dzombe, moto wonyambita, ndi cingwe: colungamitsa ciriri

1 Ambuye Yehova anandionetsa cotere; ndipo taonani, anaumba dzombe, poyamba kuphuka kwa maudzu a cibwereza; ndipo taonani, ndico cibwereza atawasengera mfumu.

2 Ndipo kunacitika m'mene lidatha kudya msipu wa dziko, ndinati, Ambuye Yehova, khululukiranitu Yakobo; adzakhala ciriri bwanji? popeza ndiye wamng'ono.

3 Ndipo Yehova anacileka. Sicidzacitika, ati Yehova.

4 Ambuye Yehova anandionetsa cotere; ndipo taonani, Ambuye Yehova anaitana kuti atsutse ndi moto; ndipo unanyambita cakudya cacikuru ukadanyambitanso dziko.

5 Pamenepo ndinati, Ambuye Yehova, Iekanitu; Yakobo adzakhala ciriri bwanji? pakuti ali wamng'ono.

6 Ndipo Yehova anacileka. Ici comwe sicidiacitika, ati Ambuye Yehova.

7 Anandionetsa cotere; ndipo taonani, Ambuye anaima pa khoma lomangiwda ndi cingwe colungamitsira ciriri; ndi cingwe colungamitsira ciriri m'dzanja lace.

8 Ndipo Yehova anati kwa ine, Amosi, uona ciani? Ndipo ndinati, Cingwe colungamitsira ciriri. Nati Ambuye, Taona, ndidzaika cingwe colungamitsira ciriri pakati pa anthu anga Israyeli, sindidzawalekanso:

9 ndi misanje ya Isake idzakhala bwinja; ndi malo opatulika a Israyeli adzapasuka; ndipo ndidzaukira nyumba ya Yerobiamu ndi lupanga.

Amosi ndi Amaziya atsutsana ku Beteli

10 Pamenepo Amaziya wansembe wa ku Beteli anatumiza kwa Yerobiamu mfumu ya Israyeli, ndi kuti, Amosi wapangira inu ciwembu pakati pa nyumba ya Israyeli; dziko silikhoza kulola mau ace onse.

11 Pakuti atero Amosi, Yerobiamu adzafa ndi lupanga, ndi Israyeli adzatengedwadi ndende, kucoka m'dziko lace.

12 Amaziya anatinso kwa Amosi, Mlauli iwe, coka, thawira ku dziko la Yuda, nudye, nunenere komweko;

13 koma usaneneranso ku Beteli; pakuti pamenepo mpa malo opatulika a mfumu, ndiyo nyumba yacifumu.

14 Pamenepo Amosi anayankha, nati kwa Amaziya, Sindinali mneneri, kapena mwana wa mneneri, koma ndinali woweta ng'ombe, ndi wakuchera nkhuyu;

15 ndipo Yehova ananditenga ndirikutsata nkhosa, nati kwa ine Yehova, Muka, nenera kwa anthu anga Israyeli.

16 Cifukwa cace tsono, tamvera mau a Yehova, Iwe ukuti, Usamanenera cotsutsana ndi Israyeli, usadonthetsa mau akutsutsana ndi nyumba ya Isake;

17 cifukwa cace atero Yehova, Mkazi wako adzakhala wadama m'mudzi, ndi ana ako amuna ndi akazi adzagwa ndi lupanga, ndi dziko lako lidzagawanidwa ndi kuyesa cingwe, ndi iwe mwini udzafa m'dziko lodetsedwa; ndipo Israyeli adzatengedwadi ndende kucoka m'dziko lace.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9