Amosi 6 BL92

Aisrayeli otsata zilakolako zao adzapsinjika ndi mtundu wina wa anthu

1 Tsoka osalabadirawo m'Ziyoni, ndi iwo okhazikika m'phiri la Samariya, ndiwo anthu omveka amtundu woposa wa anthu, amene nyumba ya Israyeli iwafikira!

2 Pitani ku Kaline, nimuone; kucokera komweko mupite ku Hamati wamkulu mutsikire ku Gati wa Afilisti; kodi awo ndi okoma koposa maufumu ano? kapena malire ao aposa malire anu?

3 Inu akutalikitsa tsiku loipa, ndi kusendeza pafupi mpando waciwawa;

4 ogona pa makama aminyanga, nadzithinula pa maguwa ao ogonapo, nadya ana a nkhosa a ku zoweta, ndi ana a ng'ombe ocoka pakati pa khola;

5 akungoyimba kutsata maliridwe a zeze, nadzilingiririra zoyimbira nazo Ingati Davide;

6 akumwera vinyo m'zipanda, nadzidzoza ndi mafuta abwino oposa, osagwidwa cisoni ndi kutyoka kwa Yosefe.

7 Cifukwa cace tsono, adzatengedwa ndende ndi oyamba kutengedwa ndende; ndi phokoso la iwo odzithinula lidzapita.

8 Ambuye Yehova walumbira pali Iye mwini, ati Yehova Mulungu wa makamu, Ndinyansidwa nako kudzikuza kwa Yakobo, ndidana nazo nyumba zace zacifumu; m'mwemo ndidzapereka mudzi, ndi zonse ziri m'menemo.

9 Ndipo kudzacitika, mukatsala amuna khumi m'nyumba imodzi, adzafa.

10 Ndipo mbalewace wa munthu akamnyamula, ndiye womtentha, kuturutsa mafupa m'nyumba, nakati kwa iye ali m'kati mwa nyumbamo, Atsala wina nawe kodi? nakati, lai; pamenepo adzati, Khala cete; pakuti sitingachule dzina la Yehova.

11 Pakuti taonani, Yehova walamulira, nadzakantha nyumba yaikuru icite mpata, ndi nyumba yaing'ono icite mindala.

12 Kodi akavalo adzathamanga pathanthwe? kodi adzalimako ndi ng'ombe? pakuti mwasanduliza ciweruzo cikhale ndulu, ndi cipatso ca cilungamo cikhale civumulo;

13 inu okondwera naco copanda pace, ndi kuti, Kodi sitinadzilimbitsa tokha mwa mphamvu yathu yathu?

14 Pakuti taonani, ndidzakuutsirani mtundu wa anthu, nyumba ya Israyeli, ati Yehova Mulungu wa makamu; ndipo adzakupsinjani kuyambira polowera ku Hamati kufikira mtsinje wa kucidikha.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9