Yoweli 2 BL92

Cilango coopsa ca Mulungu

1 Muombe lipenga m'Ziyoni, nimupfuulitse m'phiri langa lopatulika; onse okhala m'dziko anjenjemere; pakuti tsiku la Yehova lirinkudza, pakuti liyandikira;

2 tsiku la mdima, la mdima wandiweyani, tsiku la mitambo, mitambo yocindikira, ngati m'mbandakuca moyalika pamapiri; mtundu waukuru ndi wamphamvu, panalibe wotere ndi kale lonse, sipadzakhalanso wotere utapita uwu, kufikira zaka za mibadwo yambiri.

3 Moto unyambita pamaso pao, ndi m'mbuyo mwao litentha lawi la moto; kumaso kwao dziko likunga munda wa Edeni, koma m'mbuyo mwao likunga cipululu copanda kanthu; palibenso wakuwapulumuka.

4 Maonekedwe ao aoneka ngati akavalo, nathamanga ngati akavalo a nkhondo.

5 Atumphako ngati mkokomo wa magareta pamwamba pa mapiri, ngati kulilima kwa malawi a moto akupsereza ziputu, ngati mtundu wamphamvu wa anthu ondandalikira nkhondo.

6 Pamaso pao mitundu ya anthu ikumva zowawa, nkhope zonse zitumbuluka.

7 Athamanga ngati amphamvu; akwera linga ngati anthu a nkhondo; niliyenda liri lonse njira yace, osasokonezeka m'mabande ao.

8 Sakankhana, ayenda liri lonse m'mopita mwace; akagwa m'zida, siityoka nkhondo yao.

9 Alumphira mudzi, athamanga palinga, akwerera nyumba, alowera pamazenera ngati mkhungu.

10 Dziko lapansi linjenjemera pamaso pao, thambo ligwedezeka, dzuwa ndi mwezi zada, ndi nyenyezi zi'bweza kuwala kwao;

11 ndipo Yehova amveketsa mau ace pamaso pa khamu lace la nkhondo; pakuti a m'cigono mwace ndi ambirimbiri; pakuti Iye wakucita mau ace ndiye wamphamvu ndithu; pakuti tsiku la Yehova ndi lalikuru ndi loopsa ndithu; akhoza kupirira nalo ndani?

12 Koma ngakhale tsopano, ati Yehova, munditembenukire Ine ndi mtima wanu wonse, ndi kusala, ndi kulira, ndi kucita maliro;

13 ndipo ng'ambani mitima yanu, si zobvala zanu ai; ndi kurembenukira kwa Yehova Mulungu wanu; pakuti Iye ndiye wacisomo, ndi wodzala cifundo, wosapsa mtima msanga, ndi wocuruka kukoma mtima, ndi woleka coipaco.

14 Kaya, kapena adzabwerera, nadzalekerera, ndi kusiya mdalitso pambuyo pace, ndiwo nsembe yaufa ndi nsembe yathira ya Yehova Mulungu wanu.

15 Ombani lipenga m'Ziyoni, patulani tsiku losala, lalikirani msonkhano woletsa,

16 sonkhanitsani anthu, patulani msonkhano, memezani akulu akulu, sonkhanitsani ana ndi oyamwa mawere; mkwati aturuke m'cipinda mwace, ndi mkwatibwi m'mogona mwace.

17 Ansembe, atumiki a Yehova, alire pakati pa khonde la pakhomo ndi guwa la nsembe, nanene, Alekeni anthu anu, Yehova, musapereka colowa canu acitonze, kuti amitundu awalamulire; adzaneneranji mwa anthu, Ali kuti Mulunguwao?

Lonjezo lakuti cidzacuruka cakudya

18 Pamenepo Yehova anacitira dziko lace nsanje, nacitira anthu ace cifundo.

19 Ndipo Yehova anayankha, nati kwa anthu ace, Taonani, ndidzakutumizirani tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta; ndipo mudzakhuta ndi izo; ndipo sindidzakuperekaninso mukhale citonzo mwa amitundu;

20 koma ndidzakucotserani kutali nkhondo ya kumpoto, ndi kulingira ku dziko louma ndi lopasuka, a kumaso kwace ku nyanja ya kum'mawa, ndi a kumbuyo kwace ku nyanja ya kumadzulo; ndi kununkha kwace kudzakwera, ndi pfungo lace loipa lidzakwera; pakuti inacita zazikuru.

21 Usaopa, dziko iwe; kondwera, nusekerere; pakuti Yehova wacita zazikuru.

22 Musamaopa, nyama za kuthengo inu; pakuti m'cipululu muphukanso msipu; pakuti mitengo ibala zipatso zao; mikuyu ndi mipesa ipatsa mphamvu zao.

23 Mukondwere tsono, inu ana a Ziyoni, nimusekerere m'Yehova Mulungu wanu; pakuti adzayamba kukupatsani mvula yamyundo, monga mwa cilungamo cace; nakubvumbitsirani mvula, mvula yamyundo ndi yamasika mwezi woyamba.

24 Ndipo madwale adzakhala ndi tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta; zidzasefuka m'zosungiramo zao.

25 Ndipo ndidzakubwezerani zaka zidazidya dzombe, ndi cirimamine, ndi anoni, ndi cimbalanga, gulu langa lalikuru la nkhondo, limene ndinalitumiza pakati pa inu.

26 Ndipo mudzadyaidya ndi kukhuta, nimudzalemekeza dzina la Yehova Mulungu wanu, amene anacita nanu modabwiza; ndi anthu anga sadzacita manyazi nthawi zonse.

27 Ndipo mudzadziwa kuti Ine ndiri pakati pa Israyeli, ndi kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu, palibe wina; ndi anthu anga sadzacita manyazi nthawi zonse.

28 Ndipo kudzacitika m'tsogolo mwace, ndidzatsanulira mzimu wanga pa anthu onse, ndi ana anu amuna ndi akazi adzanenera, akulu akulu anu adzalota maloto, anyamata anu adzaona masomphenya;

29 ndi pa akapolo ndi adzakazi omwe ndidzatsanulira mzimu wanga masiku awo.

30 Ndipo ndidzaonetsa zodabwiza kuthambo ndi pa dziko lapansi, mwazi, ndi moto, ndi utsi tolo.

31 Dzuwa lidzasanduka mdima, ndi mwezi udzasanduka mwazi, lisanadze tsiku la Yehova lalikuru ndi loopsa.

32 Ndipo kudzacitika kuti ali yense adzaitana pa dzina la Yehova adzapulumutsidwa; pakuti m'phiri la Ziyoni ndi m'Yerusalemu mudzakhala cipulumutso, monga Yehova anatero, ndi mwa otsala amene Yehova adzawaitana.

Mitu

1 2 3