7 Unaonongadi mpesa wanga, nunyenya mkuyu wanga, nuukungudza konse, nuutaya; nthambi zace zasanduka zotumbuluka.
8 Lirani ngati namwali wodzimangira m'cuuno ciguduli, cifukwa ca mwamuna wa unamwali wace.
9 Nsembe yaufa ndi nsembe yothira zalekeka ku nyumba ya Yehova; ansembe, atumiki a Yehova, acita maliro.
10 M'munda mwaonongeka, nthaka ilira; pakuti tirigu waonongeka, vinyo watsopano wamwelera, mafuta akudza pang'onong'ono.
11 Gomani, akulima m'minda inu; lirani, akulima mpesa; cifukwa ca tirigu ndi barele; pakuti dzinthu za m'minda zatayika.
12 Mpesa wauma, mkuyu wafota, mtengo wa mkangaza ndi kanjedza ndi muula, inde mitengo yonse ya kuthengo yafota; pakuti cimwemwe cathera ana a anthu.
13 Mudzimangire ciguduli m'cuuno mwanu, nimulire ansembe inu; bwnani, otumikira ku guwa la nsembe inu; lowani, gonani usiku wonse m'ciguduli, inu otumikira Mulungu wanga; pakuti nsembe yaufa ndi nsembe yothira zaletsedwera nyumba ya Mulungu wanu.