7 Khala cete pamaso pa Ambuye Yehova; pakuti tsiku la Yehova liyandikira; pakuti Yehova wakonzeratu nsembe, anapatula oitanidwa ace.
8 Ndipo kudzacitika tsiku la nsembe ya Yehova, kuti ndidzalanga akalonga ndi ana a mfumu, ndi onse akubvala cobvala cacilendo.
9 Ndipo tsiku ilo ndidzalanga olumpha ciundo, nadzaza nyumba ya mbuye wao ndi ciwawa ndi cinyengo.
10 Ndipo tsiku ilo, ati Yehova, kudzakhala phokoso lakulira locokera ku cipata cansomba, ndi kucema kocokera ku dera laciwiri, ndi kugamuka kwakukuru kocokera kuzitunda.
11 Cemani okhala m'cigwa, pakuti amalonda onse atayika, onsewo osenza siliva aonongeka.
12 Ndipo kudzacitika nthawi yomweyi kuti ndidzasanthula Yerusalemu ndi nyali, ndipo ndidzalanga amunawo okhala ndi nsenga, onena m'mtima mwao, Yehova sacita cokoma, kapena kucita coipa.
13 Ndipo zolemera zao zidzakhala zakufunkhidwa; ndi nyumba zao zabwinja; adzamangadi nyumba, koma sadzagonamo; adzanka minda yampesa koma sadzamwa vinyo wace.