1 Pakuti, abale, mudziwa nokha malowedwe athu a kwa inu, kuti sanakhala opanda pace;
2 koma tingakhale tidamva zowawa kale, ndipo anaticitira cipongwe, monga mudziwa, ku Filipi, tinalimbika pakamwa mwa Mulungu wathu kulankhula ndi inu Uthenga Wabwino wa Mulungu m'kutsutsana kwambiri.
3 Pakuti kudandaulira kwathu sikucokera kukusocera, kapena kucidetso, kapena m'dnyengo;
4 komatu monga Mulungu anatibvomereza kutiikiza Uthenga Wabwino, kotero tilankhula; osati monga okondweretsa anthu, koma Mulungu; amene ayesa mitima yathu.