1 Atesalonika 5 BL92

1 Koma za nthawizo ndi nyengozo, abale, sikufunika kuti tidzakulemberani,

2 Pakuti inu nokha mudziwa bwino kuti tsiku la Ambuye lidzadza monga mbala usiku,

3 Pamene angonena, Mtendere ndi mosatekeseka, pamenepo cionongeko cobukapo cidzawagwera, monga zowawa mkazi wa pakati; ndipo sadzapulumuka konse.

4 Kama inu, abale, simuli mumdima, kuti tsikulo likakugwereni monga mbala;

5 pakuti inu nonse muli ana a kuunika, ndi ana a usana; sitiri a usiku, kapena a mdima;

6 cifukwa cace tsono tisagone monga otsalawo, komatu tidikire, ndipo tisaledzere,

7 Pakuti iwo akugona agona usiku; ndi iwo akuledzera aledzera usiku.

8 Koma ife popeza tiri a usana tisaledzere, titabvala capacifuwa ca cikhulupiriro ndi cikondi; ndi cisoti ciri ciyembekezo ca cipulumutso.

9 Pakuti Mulungu sanatiika ife tilawe mkwiyo, komatu kuti tilandire cipulumutso mwa Ambuye wathu Yesu Kristu,

10 amene anafa m'malo mwathu, kuti, tingakhale tidikira, tingakhale tigona, tikakhale ndi moyo pamodzi ndi Iye.

11 Mwa ici cenjezanani, ndipo mangiriranani wina ndi mnzace, monganso mumacita,

Malangizo

12 Koma, abale, tikupemphani, dziwani iwo akugwiritsa nchito mwa inu, nakhala akulu anu mwa Ambuye, nakuyatnbirirani inu;

13 ndipo muwacitire ulemu woposatu mwa cikondi, cifukwa ca nchito yao. Khalani mumtendere mwa inu nokha.

14 Koma tidandaulira inu abale, yambirirani ampwayi, limbikitsani amantha mtima? cirikizani ofok a, mukhale oleza mtima pa onse.

15 Penyani kuti wina asabwezere coipa womcitira coipa; komatu nthawi zonse mutsatire cokoma, kwa anzanu, ndi kwa onse.

16 Kondwerani nthawi zonse;

17 Pempherani kosaleka;

18 M'zonse yamikani; pakuti ici ndi cifuniro ca Mulungu ca kwa inu, mwa Kristu Yesu.

19 Musazime Mzimuyo;

20 Musanyoze maaenero;

21 Yesani zonse; sungani cokomaco,

22 Mupewe maonekedwe onse a coipa.

23 Ndipo Mulungu wa mtendere yekha ayeretse inu konsekonse; ndipo mzimu wanu ndi moyo wanu ndi thupi lanu zisungidwe zamphumphu, zopanda cirema pa kudza kwace kwa: Ambuye wathu Yesu Kristu.

24 Wakuitana inu ali wokhulupirika, amenensoadzacicita.

25 Abale, z tipempherereni ife.

26 1 Lankhulani abale onse ndi cipsompsono copatulika.

27 Ndikulumbirirani pa Ambuye kuti 2 kalatayu awerengedwe kwa abale onse.

28 Cisomo ca Ambuye wathu Yesu Kristu cikhale nanu.

Mitu

1 2 3 4 5