1 Atesalonika 3 BL92

1 Cifukwa cace, posakhoza kulekereranso, tidabvomereza mtima atisiye tokhaku Atene;

2 ndipo tinatuma Timoteo, mbale wathuyo ndi mtumiki wa Mulungu m'Uthenga Wabwino wa Kristu, kuti akhazikitse inu; ndi kutonthoza inu za cikhulupiriro canu;

3 kuti asasunthike wina ndi zisautso izi, pakuti mudziwa nokha kuti adatiika ife ticite izi.

4 Pakutinso, pamenetinali ndi inu tinakuuziranitu kuti tidzamva zisautso; monga kudacitika, monganso mudziwa.

5 Mwa ici inenso, posalekereranso, ndinatuma kukazindikira cikhulupiriro canu, kuti kaperta: woyesa akadakuyesani, ndipo cibvuto cathu cikadakhala copanda pace.

6 Koma tsopano pofika Timoteo kwathu kucokera kwa inu, ndi kutifotokozera mbiri yokoma ya cikhulupiriro ndi cikondano canu, ndi kuti mutikumbukila bwino masiku onse, pokhumba kutiona ife, monganso ire kukuonani inu;

7 cifukwa ca ici tasangalala pa inu, abale, m'kupsinjika kwathu konse ndi cisautso cathu conse, mwa cikhulupiriro canu;

8 pakuti tsopano tiri ndi moyo, ngati inu mucirimika mwa Ambuye.

9 Pakuti tikhoza kubwezera kwa Mulungu ciyamiko canji cifukwa ca inu, pa cimwemwe conse tikondwera naco mwa inu pamaso pa Mulungu wathu;

10 ndi kucurukitsa mapemphero athu usiku ndi usana kuti tikaone nkhope yanu, ndi kukwaniritsa zoperewera pa cikhulupiriro canu?

11 Koma Mulungu Atate wathu mwini yekha, ndi Ambuye wathu Yesu atitsogolere m'njira yakufika kwa inu;

12 koma Ambuye akukulitseni inu, nakueurukitseni m'cikondano wina kwa mnzace ndi kwa anthu onse, monganso ife titero kwa inu;

13 kuti akakhazikitse mitima yanu yopanda cifukwa m'ciyero pamaso pa Mulungu Atate wathu, pakufika Ambuye wathu Yesu pamodzi ndi oyera mtima ace onse.

Mitu

1 2 3 4 5