1 Pakuti, abale, mudziwa nokha malowedwe athu a kwa inu, kuti sanakhala opanda pace;
2 koma tingakhale tidamva zowawa kale, ndipo anaticitira cipongwe, monga mudziwa, ku Filipi, tinalimbika pakamwa mwa Mulungu wathu kulankhula ndi inu Uthenga Wabwino wa Mulungu m'kutsutsana kwambiri.
3 Pakuti kudandaulira kwathu sikucokera kukusocera, kapena kucidetso, kapena m'dnyengo;
4 komatu monga Mulungu anatibvomereza kutiikiza Uthenga Wabwino, kotero tilankhula; osati monga okondweretsa anthu, koma Mulungu; amene ayesa mitima yathu.
5 Pakuti sitinayenda nao mau osyasyalika nthawi iri yonse, monga mudziwa, kapena kupsiniira msiriro, mboni ndi Mulungu;
6 kapena sitinakhala ofuna ulemerero wa kwa anthu, kapena kwa inu, kapena kwa ena, tingakhale tinali nayo mphamvu yakukulemetsanl monga atumwi a Kristu.
7 Komatu tinakhala ofat sa pakati pa inu, monga m'mene mlezi afukata ana ace a iye yekha;
8 kotero ife poliralira inu, tinabvomera mokondwera kupereka kwa inu si Uthenga Wabwino wa Mulungu wokha, komanso moyo wathu, popeza mudakhala okondedwa kwa ife.
9 Pakuti mukumbukila, abale, cigwiritso cathu ndi cibvuto cathu; pocita usiku ndi usana, kuti tingalemetse wina wa inu, tinalalikira kwa inu Uthenga Wabwino wa Mulungu.
10 Inu ndinu mboni, Mulungunso, kuti tinakhala oyera mtima ndi olungama ndi osalakwa kwa inu akukhulupirira;
11 monga mudziwa kuti tinacitira yense wa inu pa yekha, monga atate acitira ana ace a iye yekha, ndi kukudandaulirani, ndi kukusangalatsani ndi kucita umboni,
12 kuti muyende koyenera Mulungu, amene akuitanani inu mulowe ufumu wace wa iye yekha, ndi ulemerero.
13 Ndipo mwa icinso ife tiyamika Mulungu kosalekeza, kuti, pakulandira mau a Uthenga wa Mulungu, simunawalandira monga mau a anthu, komatu monga momwe ali ndithu, mau a Mulungu, amenenso acita mwa inuokhulupirira.
14 Pakuti inu, abale, munayamba kukhala akutsanza a Mipingo ya Mulungu yokhala m'Yudeya mwa Kristu Yesu; popeza zomwezi mudazimva kowawa nelinunso pamanja pa a mtundu wanu wa inu nokha, monganso iwowapa manja a Ayuda;
15 amene adaphanso Ambuye Yesu, ndi aneneri, natilondalonda ife, ndipo sakondweretsa Mulungu, natsutsana nao anthu onse;
16 natiletsa ife kuti tisalankhule ndi akunja kuti apulumutsidwe; kudzaza macimo ao nthawi zonse; koma mkwiyo wafika pa iwo kufikira cimariziro.
17 Koma ife, abale, angakhale adaticotsa kusiyana nanu kanthawi, osapenyana maso, koma kusiyana mtima ai, tinayesetsa koposa kuona nkhope yanu ndi cilakolako cacikuru;
18 cifukwa tinafuna kudza kwa inu, inedi Paulo ndatero kamodzi kapena kawiri; koma Satana anatiletsa.
19 Pakuti ciyembekezo cathu, kapena cimwemwe, kapena korona wakudzitamandira naye nciani? si ndinu nanga pamaso pa Ambuye wathu Yesu m'kufika kwace?
20 Pakuti inu ndinu ulemerero wathu ndi cimwemwe cathu.