2 Atesalonika 1 BL92

1 PAULO, ndi Silvano, ndi Timoteo, kwa Mpingo wa Atesalonika mwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye Yesu Kristu:

2 Cisomo kwa inu ndi mtendere wa kwa Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Kristu.

Kulimbika kwa Atesalonika nkana asautsidwa

3 Tiziyamika Mulungu nthawi zonse cifukwa ca inu, abale, monga kuyenera; pakuti cikhulupiriro canu cikula cikulire, ndipo cicurukira cikondanoca inu nonse, yense pa mnzace;

4 kotero kuti ife tokha tidzitamandira za inu m'Mipingo ya Mulungu, cifukwa ca cipiriro canu, ndi cikhulupiriro canu, m'mazunzo anu onse ndi zisautsozo muzimva;

5 ndico citsimikizo ca ciweruziro colungama ca Mulungu; kuti mu-kawerengedwe oyenera ufumu wa Mulungu, umenenso mumvera zowawa;

6 popeza nkolungama kwa Mulungu kubwezera cisautso kwa iwo akucitira inu cisautso,

7 ndi kwa inu akumva cisautso mpumulo pamodzi ndi ire, pa bvumbulutso la Ambuye Yesu wocokera Kumwamba pamodzi ndi angelo a mphamvu yace,

8 m'lawi lamoto, ndi kubwezera cilango kwa iwo osamdziwa Mulungu, ndi iwo osamvera Uthenga Wabwino wa Ambuye wathu Yesu;

9 amene adzamva cilango, ndico cionongeko cosatha cowasiyanitsa ku nkhope ya Ambuye, ndi ku ulemerero wa mphamvu yace,

10 pamene adzadza kudzalemekezedwa mwa oyera mtima ace, ndi kukhala wodabwizitsa mwa onse akukhulupirira (popeza munakhulupirira umboni wathu wa kwa inu) m'tsiku lija.

11 Kukatero tikupemphereraninso nthawi zonse, kuti Mulungu wathu akakuyeseni inu oyenera kuitanidwa kwanu, nakakwaniritse comkomera conse, ndi nchito ya cikhulupiriro mumphamvu;

12 kuti dzina la Ambuye wathu Yesu lilemekezedwe mwa inu, ndi inu mwa iye, monga mwa cisomo ca Mulungu wathu ndi Ambuye Yesu Kristu.

Mitu

1 2 3