1 Cotsalira, abale, mutipempherere, kuti mau a Ambuye athamange, nalemekezedwe, monganso kwanu;
2 ndi kuti tilanditsidwe m'manja a anthu osayenerandi oipa; pakuti si onse ali naco cikhulupiriro.
3 Koma Ambuye ali wokhulupirika amene adzakukhazikitsani inu, nadzakudikirirani kuletsa woipayo;
4 koma tikhulupirira mwa Ambuye za inu, kuti mumacita, ndiponso mudzacita zimene tikulamulirani.
5 Ndipo Ambuye atsogolere bwino mitima yanu ilowe m'cikondi ca mulungu ndi m'cipiriro ca Kristu,
6 Ndipo tikulamulirani, abale, m'dzina la Ambuye wathu Yesu Kristu, kuti mubwebvuke kwa mbale yense wakuyenda dwacedwace, wosatsata mwambo umene anaulandira kwa ife.
7 Pakuti mudziwa nokha m'mene muyenera kutitsanza ifemo; pakuti sitinakhala dwacedwace mwa inu;
8 kapena sitinadya mkate cabe pa dzanja la munthu ali yense, komatu m'cibvuto ndi cipsinjo, tinagwira nchito usiku ndi usana, kuti tingalemetse wina wa inu;
9 si cifukwa tiribe ulamuliro, komatu kuti tidzipereke tokha tikhale kwa inu citsanzo canu, kuti mukatitsanze ife.
10 Pakutinso pamene tinali nanu tidakulamulirani ici, Ngati munthu safuna kugwira nchito, asadyenso.
11 Pakuti tikumva za ena mwa inu kuti ayenda dwacedwace, osagwira nchito konse, kama ali ocita mwina ndi mwina.
12 Koma oterewa tiwalamulira ndi kuwadandaulira mwa Ambuye Y esu Kristu, kuti agwire nchito pokhala cete, nadye cakudya cadwo okha,
13 Kama inu, abale, musaleme pakucita zabwino.
14 Koma ngati wina samvera mau athu m'kalata uyu, yang'anirani ameneyo, kuti musayanjane naye, kuti acite manyazi.
15 Koma musamuyese mdani, kama mumuyambirire ngati mbale.
16 Ndipo Ambuye wa mtendere yekha atipatse ife mtendere nthawi zonse, monsemo. Ambuye akhale ndi inu nonse.
17 Cilankhulo ndi dzanja langa Paulo; ndico cizindikilo m'kalata ali yense; ndiko kulemba kwanga.
18 Cisomo ca Ambuye wathu Yesu Kristu cikhale ndi inu nonse.