1 Timoteo 1 BL92

Paulo alangiza Timoteo

1 PAULO, mtumwi wa Kristu Yesu monga mwa cilamuliro ca Mulungu Mpulumutsi wathu, ndi ca Kristu Yesu, ciyembekezo cathu:

2 kwa Timoteo mwana wanga weniweni m'cikhulupiriro: Cisomo, cifundo, mtendere za kwa Mulungu Atate ndi kwa Kristu Yesu Ambuye wathu.

3 Monga ndinakudandaulira iwe utsalire m'Efeso, popita ine ku Makedoniya, nditeronso, kuti ukalamulire ena ajawa asaphunzitse kanthu kena,

4 kapena asasamale nkhani zacabe, ndi mawerengedwe osalekeza a mafuko a makolo, ndiwo akuutsa mafunso, osati za udindo wa Mulungu umene uli m'cikhulupiriro;

5 koma citsirizo ca cilamuliro ndico cikondi cocokera mu mtima woyera ndi m'cikumbu mtima cokoma ndi cikhulupiriro cosanyenga;

6 zimenezo, ena pozilambalala anapatukira kutsata mau opanda pace;

7 pofuna kukhala aphunzitsi a lamulo ngakhale sadziwitsa zimene azmena, kapena azilimbikirazi.

8 Koma mudziwa kuti lamulo ndi labwino, ngati munthu acita nalo monga mwa lamulo,

9 podziwa ici, kuti lamulo siliikika kwa munthu wolungama, koma kwa osayeruzika ndi osamvera lamulo, osapembedza, ndi ocimwa, osalemekeza ndi amnyozo, akupha atate ndi akupha amai, akupha anzao,

10 acigololo, akucita zoipa ndi amuna, akuba anthu, amabodza, olumbira zonama, ndipo ngati kuli kena kakutsutsana naco ciphunzitso colamitsa;

11 monga mwa Uthenga Wabwino wa ulemerero wa Mulungu wolemekezeka, umene anandisungitsa ine.

12 Ndimyamika iye wondipatsa ine mphamvu, ndiye Kristu Yesu, Ambuye wathu, kuti anandiyesa wokhulupirika, nandiika kuutumiki,

13 ndingakhale kale ndinali wamwano, ndi wolondalonda, ndi wacipongwe; komatu anandicitira cifundo, popeza ndinazicita wosazindikira, wosakhulupirira;

14 koma cisomo ca Ambuye wathu cidacurukatu pamodzi ndi cikhulupiriro ndi cikondi ciri mwa Kristu Yesu.

15 Mauwa ali okhulupirika ndi oyenera konse kuti awalandire, kuti Kristu Yesu anadza ku dziko lapansi kupulumutsa ocimwa; wa iwowa ine ndine woposa;

16 komatu mwa ici anandicitira cifundo, kuti mwa ine, woyamba, Yesu Kristu akaonetsere kuleza mtima kwace konse kukhale citsanzo ca kwa iwo adzakhulupirira pa iye m'tsogolo kufikira moyo wosatha.

17 Ndipo kwa Mfumu yosatha, yosabvunda, yosaoneka, Mulungu wa yekha, ukhale ulemu ndi ulemerero, kufikira nthawi za nthawi. Amen.

18 Lamulo ili ndipereka kwa iwe, mwana wanga Timoteo, kuti, emonga mwa zonenera zidakutsogolera iwe kale, ulimbane nayo nkhondo yabwino;

19 ndi kukhala naco cikhulupiriro ndi cikumbu mtima cokoma, cimene ena adacikankha, cikhulupiriro cao cidatayika;

20 a iwo ali Humenayo ndi Alesandro, amene ndawapereka kwa Satana, kuti aphunzire kusalankhula zamwano.

Mitu

1 2 3 4 5 6