1 Timoteo 5 BL92

Za okalamba ndi amasiye

1 Mkulu usamdzudzule, komatu umdandaulire ngati atate; anyamata ngati abale;

2 akazi akulu ngati amai; akazi ang'ono ngati alongo, m'kuyera mtima konse.

3 Citira ulemu amasiye amene ali amasiye ndithu.

4 Koma ngati wamasiye wina ali nao ana kapena adzukulu, ayambe aphunzire iwo kucitira ulemu a m'banja lao, ndi kubwezera akuwabala; pakuti ici ncolandirika pamaso pa Mulungu.

5 Koma iye amene ali wamasiye ndithu, nasiyidwa yekha, ayembekezera Mulungu, nakhalabe m'mapembedzo ndi mapemphero usiku ndi usana.

6 Koma iye wakutsata zomkondweretsa, adafa pokhala ali ndi moyo,

7 Ndipo izi ulamulire, kuti akhale opanda ciremao

8 Koma ngati wina sadzisungiratu mbumba yace ya iye yekha, makamaka iwo a m'banja lace, wakana cikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupira.

9 Asawerengedwe wamasiye ngati sanafikire zaka makumi asanu ndi limodzi, atakhala mkazi wa mwamuna mmodzi,

10 wa mbiri ya nchito zabwino; ngati walera ana, ngati wacereza alendo, ngati adasambitsa mapazi a nzera mtima, ngati wathapdiza osautsidwa, ngati anatsatadi nchito zonse zabwino.

11 Koma amasiyeang'ono uwakane; pakuti pamene ayambakumcitira Kristu cipongwe afuna kukwatiwa;

12 pokhala naco citsutso, popeza adataya cikhulupiriro cao coyamba.

13 Ndipo aphunziraponso kucita ulesi, aderuderu; koma osati ulesi wokha, komatunso alankhula zopanda pace, nacita mwina ndi mwina, olankhula zosayenera.

14 Cifukwa cace nditi akwatiwe amasiye ang'ono, nabale ana, naweruzire nyumba, osapatsa cifukwa kwa mdaniyo cakulalatira;

15 pakuti adayamba enakupatuka ndi kutsata Satana.

16 Ngati mkazi wina wokhulupira ali nao amasiye, iye awathandize, ndipo Mpingowo usalemedwe; kuti uthandize iwo amene ali amasiye ndithu.

Ulamuliro wa aphunzitsi; Malangizo ena

17 Akuru akuweruza bwino ayesedwe oyenera ulemu wowirikiza, makamaka iwo akucititsa m'mau ndi m'ciphunzitso.

18 Pakuti malembo ati, Usapunamiza ng'ombe yopuntha tirigu. Ndipo, Wogwira nchito ayenera kulipira kwace.

19 Pa mkulu usalandire comnenera, koma pakhale mboni ziwiri kapena zitatu.

20 Iwo akucimwa uwadzudzule pamaso pa onse, kuti otsalawo acite mantha.

21 Ndikucitira umboni pamaso pa Mulungu, ndi Kristu Yesu, ndi angelo osankhika, kuti usunge izi kopanda kusankhiratu, wosacita kanthu monga mwa tsankhu.

22 Usafulumira kuika manja pa munthu ali yense, kapena usayanjana nazo zoipa za eni; udzisunge wekha woyera mtima.

23 Usakhalenso wakumwa madzi okha, komatu ucite naye vinyo pang'ono, cifukwa ca mimba yako ndi zofoka zako zobwera kawiri kawiri.

24 Zocimwa za anthu ena ziri zooneka-kale, zitsogola kunka kumlandu; koma enanso ziwatsata.

25 Momwemonso pali nchito zokoma zinaonekera kale; ndipo zina zosati zotere sizikhoza kubisika.

Mitu

1 2 3 4 5 6