1 Timoteo 3 BL92

Zoyenera oyang'anira ndi atumiki

1 Mauwa ali okhulupirika, ngati munthu akhumba udindo wa woyang'anira, aifuna nchito yabwino.

2 Ndipo kuyenera woyang'anira akhale wopanda cirema, mwamuna wa mkazi mmodzi, wodzisunga, wodziletsa, wolongosoka, wokonda kucereza alendo, wokhoza kuphunzitsa;

3 wosati woledzera, kapena womenyana ndeu; komatu wofatsa, wopanda ndeu, wosakhumba cuma;

4 woweruza bwino nyumba yace ya iye yekha, wakukhala nao ana ace omvera iye ndi kulemekezeka konse.

5 Koma ngati munthu sadziwa kuweruza nyumba ya iye yekha, adzasunga bwanji Mpingo wa Mulungu?

6 Asakhale wophunza, kuti podzitukumula ungamgwere mlandu wa mdierekezi.

7 Kuyeneranso kuti iwo akunja adzakhoza kumcitira umboni wabwino; kuti ungamgwere mtonzo, ndi msampha wa mdierekezi.

8 Momwemonso atumiki akhale olemekezeka, osanena pawiri, osamwetsa vinyo, osati a cisiriro conyansa;

9 okhala naco cinsinsi ca cikhulupiriro m'cikumbu mtima coona.

10 Koma iwonso ayambe ayesedwe; pamenepo atumikire, akakhala opanda cifukwa.

11 Momwemonso akazi akhale olemekezeka, osadierekeza, odzisunga, okhulupirika m'zonse.

12 Atumiki akhale mwamuna wa mkazi mmodzi, akuweruza bwino ana ao, ndi iwo a m'nyumba yao ya iwo okha.

13 Pakuti iwo akutumikira bwino adzitengera okha mbiri yabwino, ndi kulimbika kwakukuru m'cikhulupiriro ca mwa Kristu Yesu.

14 Izi ndikulembera ndi kuyembekeza kudza kwa iwe posacedwa, koma ngati ndicedwa,

15 kuti udziwe kuyenedwa kwace pokhala m'nyumba ya Mulungu, ndiye Eklesia wa Mulungu wamoyo, mzati ndi mcirikizo wa coonadi.

16 Ndipo pobvomerezeka, cinsinsi ca kucitira Mulungu ulemu ncacikuru: iye amene anaonekera m'thupi, anayesedwa wolungama mumzimu, anapenyeka ndi angelo, analalikidwa mwa amitundu, wokhulupiridwa m'dziko lapansi, wolandiridwa m'ulemerero.

Mitu

1 2 3 4 5 6