1 Timoteo 2 BL92

Pempherero la kwa anthu onset

1 Ndidandaulira tsono, poyambayamba, kuti acitike mapembedzo, mapemphero, mapembedzero, mayamiko, cifukwa ca anthu onse;

2 cifukwa ca mafumu ndi onse akucita ulamuliro kuti m'moyo mwathu tikakhale odika mtima, ndi acete m'kulemekeza Mulungu, ndi m'kulemekezeka monse.

3 Pakuti ici ncokoma ndi colandirika pamaso pa Mulungu Mpulumutsi wathu;

4 amene afuna anthu onse apulumuke, nafike pozindikira coonadi.

5 Pakuti pali Mulungu mmodzi, ndi Mtetezi mmodzi pakati pa Mulungu ndi anthu, ndiye munthu, Kristu Yesu,

6 amene anadzipereka yekha ciombolom'malo mwa onse; umboni m'nyengo zace;

7 umene anandiika ine mlaliki wace ndi mtumwi (ndinena zoona, wosanama ine), mphunzitsi wa amitundu m'cikhulupiriro ndi coonadi.

8 Cifukwa cace ndifuna kuti amunawo apemphere pamalo ponse, ndi kukweza manja oyera, opanda mkwiyo ndi makani.

Zoyenera akazi

9 Momwemonso, akazi adzibveke okha ndi cobvala coyenera, ndi manyazi, ndi cidziletso; osati ndi tsitsi lace loluka, ndi golidi kapena ngale, kapena maraya a mtengo wace wapatali;

10 komatu (umo mokomera akazi akubvomereza kulemekeza Mulungu), mwa nchito zabwino.

11 Mkazi aphunzire akhale wacete m'kumvera konse.

12 Koma sindilola ine kuti mkazi aphunzitse, kapena kulamulira mwamuna; komatu akhale cete.

13 Pakuti Adamu anayamba kulengedwa, pamenepo Heva;

14 ndipo Adamu sananyengedwa, koma mkaziyo ponyengedwa analowa m'kulakwa;

15 koma adzapulumutsidwa mwa kubala mwana, ngati akhala m'cikhulupiriro ndi cikondi ndi ciyeretso pamodzi ndi cidziletso.

Mitu

1 2 3 4 5 6