1 Timoteo 4 BL92

Cipanduko ca m'masiku otsiriza

1 Koma Mzimu anena monenetsa, kuti m'masiku otsiriza ena adzataya cikhulupiriro, ndi kusamala mizimu yosoceretsa ndi maphunziro a ziwanda,

2 m'maonekedwe onyenga a iwo onena mabodza, olocedwa m'cikumbu mtima mwao monga ndi citsulo camoto;

3 akuletsa ukwati, osivitsa zakudya zakuti, zimene Mulungu anazilenga kuti acikhulupiriro ndi ozindikira coonadi azilandire ndi ciyamiko.

4 Pakuti colengedwa conse ca Mulungu ncabwino, ndipo palibe kanthu kayenera kutayika, ngati kalandiridwa ndi ciyamiko;

5 pakuti kayeretsedwa ndi Mau a Mulungu ndi kupemphera.

A utumiki akhale okhulupirika ndi acangu

6 Ngati ukumbutsa abale zinthu izi, udzakhala mtumiki wabwino wa Kristu Yesu, woleredwa m'mauwo a cikhulupiriro, ndi malangizo abwino amene udawatsata;

7 koma nkhani zacabe ndi za akazi okalamba ukane. Ndipo udzizoloweretse kucita cipembedzo;

8 pakuti cizolowezi ca thupi cipindula pang'ono, koma cipembedzo cipindula zonse, popeza cikhala nalo Lonjezano la ku moyo uno, ndi la moyo ulinkudza.

9 Okhulupirika mauwa ndi oyenera kulandiridwa konse.

10 Pakuti kukalingako tlgwiritsa nchito ndi kuyesetsa, cifukwa ciyembekezo cathu tiri naco pa Mulungu wamoyo, amene ali Mpulumutsi wa anthu onse, makamaka wa okhulupira.

11 Lamulira izi, nuziphunzitse.

12 Munthu asapeputse ubwana wako; komatu khala citsanzo kwa iwo okhulupira, m'mau, m'mayendedwe, m'cikondi, m'cikhulupiriro, m'kuyera mtima.

13 Kufikira ndidza ine, usamalire kuwerenga, kucenjeza, kulangiza.

14 Usanyalapse mphatsoyo iri mwa iwe, yopatsidwa kwa iwe mwa cinenero, pamodzi ndi kuika kwa manja a akulu.

15 Izi uzisamalitse; mu izi ukhale; kuti kukula mtima kwako kuonekere kwa onse.

16 Udzipenyerere wekha, ndi ciphunzitsoco. Uzikhala muizi; pakuti pocita ici udzadzipulumutsa iwe wekha ndi iwo akumva iwe.

Mitu

1 2 3 4 5 6