1 Ndipo tikupemphani, abale, cifukwa ca kudza kwace kwa Ambuye wathu Yesu Kristu, ndi kusonkhana pamodzi kwathu kwa iye;
2 kuti musamagwedezeka mtima msanga ndi kutaya maganizo anu, kapena kuopsedwa, mwa mzimu kapena mwa mau; kapena mwa kalata, monga wolembedwa ndi ife, monga ngati tsiku la Ambuye lafika;
3 munthu asakunyengeni konseko; kuti silifika, koma ciyambe cifike cipatukoco, nabvumbulutsike munthu wosayeruzika, mwana wa cionongeko,
4 amene atsutsana nazo, nadzikuza pa zonse zochedwa Mulungu, kapena zopembedzeka; kotero kuti iye wakhalapansi ku Kacisi wa Mulungu, nadzionetsera yekha kuti ali Mulungu.
5 Simukumbukila kodi, kuti pokhala nanu, ndisanacoke ine, ndinakuuzani izi?
6 Ndipo tsopano comletsa mucidziwa, kuti akabvumbulutsidwe iye m'nyengo yace ya iye yekha.
7 Pakuti cinsinsi ca kusayeruzika cayambadi kucita; cokhaci pali womletsa tsopano, kufikira akamcotsa pakati.
8 Ndipo pamenepo adzabvumbulutsidwa wosayeruzikayo, amene Ambuye Yesu adzamthera ndi mzimu wa pakamwa pace, nadzamuononga ndi maonekedwe a kudza kwace;
9 ndiye amene kudza kwace kuli monga mwa macitidwe a Satana, mu mphamvu yonse, ndi zizindikilo ndi zozizwa zonama;
10 ndi m'cinyengo conse ca cosalungama kwa iwo akuonongeka, popeza cikondi ca coonadi sanacisandira, kuti akapulumutsidwe iwo.
11 Ndipo cifukwa cace Mulungu atumiza kwa iwo macitidwe a kusoceretsa, kuti akhulupirire bodza;
12 kuti aweruzidwe onse amene sanakhulupirira coonadi, komatu anakondwera ndi cosalungama.
13 Koma tiyenera ife tiziyamika Mulungu nthawi zonse cifukwa: ca inu, abale okondedwa ndi Ambuye, kuti Mulungu anakusankhani inu kuyambira paciyambi, mulandire cipulumutso mwa ciyeretso ca Mzimu ndi cikhulupiriro ca coonadi;
14 kumene aoaitanako inu mwa Uthenga Wabwino wathu, kuti mulandire ulemerero wa Ambuye wathu Yesu Kristu.
15 Cifukwa cace tsono, abale, cirimikani, gwiritsani miyambo imene tinakuphunzitsani, kapena mwa mau, kapena mwa kalata wathu.
16 Ndipo Ambuye wathu Yesu Kristu, ndi Mulungu Atate wathu amene anatikonda natipatsa elsangalatso cosatha ndi ciyembekezo cokoma mwa cisomo,
17 asangalatse mitima yanu, nakhazikitse inu mu nchito yonse ndi mau onse abwino.