11 monga mudziwa kuti tinacitira yense wa inu pa yekha, monga atate acitira ana ace a iye yekha, ndi kukudandaulirani, ndi kukusangalatsani ndi kucita umboni,
12 kuti muyende koyenera Mulungu, amene akuitanani inu mulowe ufumu wace wa iye yekha, ndi ulemerero.
13 Ndipo mwa icinso ife tiyamika Mulungu kosalekeza, kuti, pakulandira mau a Uthenga wa Mulungu, simunawalandira monga mau a anthu, komatu monga momwe ali ndithu, mau a Mulungu, amenenso acita mwa inuokhulupirira.
14 Pakuti inu, abale, munayamba kukhala akutsanza a Mipingo ya Mulungu yokhala m'Yudeya mwa Kristu Yesu; popeza zomwezi mudazimva kowawa nelinunso pamanja pa a mtundu wanu wa inu nokha, monganso iwowapa manja a Ayuda;
15 amene adaphanso Ambuye Yesu, ndi aneneri, natilondalonda ife, ndipo sakondweretsa Mulungu, natsutsana nao anthu onse;
16 natiletsa ife kuti tisalankhule ndi akunja kuti apulumutsidwe; kudzaza macimo ao nthawi zonse; koma mkwiyo wafika pa iwo kufikira cimariziro.
17 Koma ife, abale, angakhale adaticotsa kusiyana nanu kanthawi, osapenyana maso, koma kusiyana mtima ai, tinayesetsa koposa kuona nkhope yanu ndi cilakolako cacikuru;