13 Koma sitifuna, abale, kuti mukhale osadziwa za iwo akugona; kuti mungalire monganso otsalawo, amene alibe ciyembekezo.
14 Pakuti ngati tikhulupirira kuti Yesu adamwalira, nauka, koteronso Mulungu adzatenga pamodzi ndi iye iwo akugona mwa Yesu.
15 Pakuti ici tinena kwa inu m'mau a Ambuye, kuti ife okhala ndi moyo, otsalira kufikira kufikanso kwa Ambuye, sitidzatsogolera ogonawo.
16 Pakuti Ambuye adzatsika Kumwamba mwini yekha ndi mpfuu, ndi mau a mngelo wamkuru, ndi lipenga la Mulungu; ndipo akufa mwa Ambuye adzayamba kuuka;
17 pamenepo ife okhala ndi moyo, otsalafe, tidzakwatulidwa nao pamodzi m'mitambo, kukakomana ndi Ambuye mumlengalenga, ndipo potero tidzakhala ndi Ambuye nthawi zonse.
18 Comweco, tonthozanani ndi mau awa,