3 Pakuti ici ndi cifuniro ca Mulungu, ciyeretso canu, kuti mudzipatule kudama;
4 yense wa inu adziwe kukhala naco cotengera cace m'ciyeretso ndi ulemu,
5 kosati m'eiliro ca cilakolako conyansa, monganso amitundu osadziwa Mulungu;
6 asapitirireko munthu, nanyenge mbale wace m'menemo, cifukwa Ambuye ndiye wobwezera wa izi zonse, monganso tinakuuziranitu, ndipo tinacitapo umboni.
7 Pakuti Mulungu sanaitana ife titsate cidetso, koma ciyeretso.
8 Cifukwa cace iye wotaya ici, sataya munthu, komatu Mulungu, wakupatsa Mzimu wace Woyera kwa inu.
9 Koma kunena za cikondano ca pa abale sikufunika kuti akulembereni; pakuti wakukuphunzitsani ndi Mulungu, kuti mukondane wina ndi mnzace;