7 Pakuti Mulungu sanaitana ife titsate cidetso, koma ciyeretso.
8 Cifukwa cace iye wotaya ici, sataya munthu, komatu Mulungu, wakupatsa Mzimu wace Woyera kwa inu.
9 Koma kunena za cikondano ca pa abale sikufunika kuti akulembereni; pakuti wakukuphunzitsani ndi Mulungu, kuti mukondane wina ndi mnzace;
10 pakutinso munawacitira ici abale onse a m'Makedoniya lonse. Koma tikudandaulirani, abale, mueurukireko koposa,
11 ndi kuti muyesetse kukhala cete ndi kucita za inu eni ndi kugwira nchito ndi manja anu, monga tinakuuzani;
12 kuti mukayende oona mtima pa iwo a kunja, ndi kukhala osasowa kanthu.
13 Koma sitifuna, abale, kuti mukhale osadziwa za iwo akugona; kuti mungalire monganso otsalawo, amene alibe ciyembekezo.