13 ndipo muwacitire ulemu woposatu mwa cikondi, cifukwa ca nchito yao. Khalani mumtendere mwa inu nokha.
14 Koma tidandaulira inu abale, yambirirani ampwayi, limbikitsani amantha mtima? cirikizani ofok a, mukhale oleza mtima pa onse.
15 Penyani kuti wina asabwezere coipa womcitira coipa; komatu nthawi zonse mutsatire cokoma, kwa anzanu, ndi kwa onse.
16 Kondwerani nthawi zonse;
17 Pempherani kosaleka;
18 M'zonse yamikani; pakuti ici ndi cifuniro ca Mulungu ca kwa inu, mwa Kristu Yesu.
19 Musazime Mzimuyo;