1 Cotsalira, abale, mutipempherere, kuti mau a Ambuye athamange, nalemekezedwe, monganso kwanu;
2 ndi kuti tilanditsidwe m'manja a anthu osayenerandi oipa; pakuti si onse ali naco cikhulupiriro.
3 Koma Ambuye ali wokhulupirika amene adzakukhazikitsani inu, nadzakudikirirani kuletsa woipayo;
4 koma tikhulupirira mwa Ambuye za inu, kuti mumacita, ndiponso mudzacita zimene tikulamulirani.
5 Ndipo Ambuye atsogolere bwino mitima yanu ilowe m'cikondi ca mulungu ndi m'cipiriro ca Kristu,
6 Ndipo tikulamulirani, abale, m'dzina la Ambuye wathu Yesu Kristu, kuti mubwebvuke kwa mbale yense wakuyenda dwacedwace, wosatsata mwambo umene anaulandira kwa ife.
7 Pakuti mudziwa nokha m'mene muyenera kutitsanza ifemo; pakuti sitinakhala dwacedwace mwa inu;