2 Ndipo ambiri adzatsata zonyansa zao; cifukwa ca iwo njira ya coonadi idzanenedwa zamwano.
3 Ndipo m'cisiriro adzakuyesani malonda ndi mau onyenga; amene ciweruzo cao sicinacedwa ndi kale lomwe, ndipo citayiko cao siciodzera.
4 Pakuti ngati Mulungu sanalekerera angelo adacimwawo, koma anawaponya kundende nawaika ku maenje a mdima, asungike akaweruzidwe;
5 ndipo sanalekerera dziko lapansi lakale, koma anasunga Nowa mlaliki wa cilungamo, ndi anzace asanu ndi awiri, pakulitengera dziko la osapembedza cigumula;
6 ndipo pakuisandutsa makara midzi ya Sodoma ndi Gomora anaitsutsa poigwetsa, ataiika citsanzo ca kwa iwo akakhala osapembedza;
7 ndipo anapulumutsa Loti wolungamayo, wolema mtima ndi mayendedwe onyansa a oipa aja
8 (Pakuti wolungamayo pokhala pakati pao, ndi kuona ndi kumva zao, anadzizunzira moyo wace wolungama tsiku ndi tsiku ndi nchito zao zosayeruzika).