1 Koma padakhalanso pakati pa anthuwo aneneri onama, monganso padzakhala aphunzitsi onama pakati pa inu, amene adzalowa nayo m'tseri mipatuko yotayikitsa, nadzakana Ambuye amene adawagula, nadzadzitengera iwo okha citayiko cakudza msanga.
2 Ndipo ambiri adzatsata zonyansa zao; cifukwa ca iwo njira ya coonadi idzanenedwa zamwano.
3 Ndipo m'cisiriro adzakuyesani malonda ndi mau onyenga; amene ciweruzo cao sicinacedwa ndi kale lomwe, ndipo citayiko cao siciodzera.
4 Pakuti ngati Mulungu sanalekerera angelo adacimwawo, koma anawaponya kundende nawaika ku maenje a mdima, asungike akaweruzidwe;
5 ndipo sanalekerera dziko lapansi lakale, koma anasunga Nowa mlaliki wa cilungamo, ndi anzace asanu ndi awiri, pakulitengera dziko la osapembedza cigumula;
6 ndipo pakuisandutsa makara midzi ya Sodoma ndi Gomora anaitsutsa poigwetsa, ataiika citsanzo ca kwa iwo akakhala osapembedza;
7 ndipo anapulumutsa Loti wolungamayo, wolema mtima ndi mayendedwe onyansa a oipa aja
8 (Pakuti wolungamayo pokhala pakati pao, ndi kuona ndi kumva zao, anadzizunzira moyo wace wolungama tsiku ndi tsiku ndi nchito zao zosayeruzika).
9 Ambuye adziwa kupulumutsa opembedza poyesedwa iwo, ndi kusunga osalungama kufikira tsiku loweruza akalangidwe;
10 kama makamaka iwo akutsata zathupi, m'cilakolako ca zodetsa, napeputsa cilamuliro; osaopa kanthu, otsata cifuniro ca iwo eni, santhunthumira kucitira mwano akulu;
11 popeza angelo, angakhale awaposa polimbitsa mphamvu, sawaneneza kwa Ambuye mlandu wakucita mwano.
12 Koma awo, ngati zamoyo zopanda nzeru, nyama zobadwa kuti zikodwe ndi kuonongedwa, akucitira mwano pa zinthu osazidziwa, adzaonongeka m'kuononga kwao,
13 ocitidwa zoipa kulipira kwa cosalungama; anthu akuyesera cowakondweretsa kudyerera usana; ndiwo mawanga ndi zirema, akudyerera m'madyerero acikondi ao, pamene akudya nanu;
14 okhala nao maso odzala ndi cigololo, osakhoza kuleka ucimo, kunyengerera iwo a moyo wosakhazikika; okhala nao mtima wozolowera kusirira; ana a temberero;
15 posiya njira yolunjika, anasokera, atatsata njira ya Balamu mwana wa Beori, amene anakonda mphotho ya cosalungama;
16 koma anadzudzulidwa pa kulakwa kwace mwini; buru wopanda mau, wolankhula ndi mau a munthu, analetsa kuyarukakwa mneneriyo.
17 Iwo ndiwo akasupe opanda madzi, nkhungu yokankhika ndi mkuntho; amene iadima wakuda bii uwasungikira,
18 Pakuti polankhula mau otukumuka opanda pace, anyengerera pa zilakolako za thupi, ndi zonyansa, iwo amene adayamba kupulumukira a mayendedwe olakwawo;
19 ndi kuwalonjezera iwo ufulu, pokhala iwo okha ali aka polo a cibvundi; pakuti iye amene munthu agonjedwa naye, ameneyonso adzakhala kapolo wace.
20 Pakuti ngati, adatha kuthawa zodetsa za dziko lapansi mwa cizindikiritsoca, Ambuye ndi Mpulumutsi Yesu Kristu, akodwanso nazo, nagonjetsedwa, zorsiriza zao zidzaipa koposa zoyambazo,
21 Pakuti pakadakhala bwino kwa iwo akadakhala osazindikira njira ya cilungamo, ndi poizindikira, kubwerera kutaya lamulo lopatulika lopatsidwa kwa iwo.
22 Cidawayenera iwo ca nthanthi yoona, Garu wabwerera ku masanzi ace, ndi nkhumba idasambayi yabwerera kukunkhulira m'thope.