2 Petro 3 BL92

Kubwera kwa Ambuye

1 Okondedwa, uyu ndiye kalata waciwiri ndilembera kwa inu tsopano; mwa onse awiri nditsitsimutsa mtima wanu woona ndi kukukumbutsani;

2 kuti mukumbukile mau onenedwa kale ndi aneneri oyera, ndi lamulo la Ambuye ndi Mpulumutsi, mwa atumwi anu;

3 ndi kuyamba kucizindikira ici kuti masiku otsiriza adzafika onyoza ndi kucita zonyoza, oyenda monga mwa zilakolako za iwo eni,

4 ndi kunena, Liri kuti lonjezano la kudza kwace? pakuti kuyambira kuja makolo adamwalira zonse zikhala monga ciyambire cilengedwe.

5 Pakuti ici aiwala dala, kuti miyamba inakhala kale lomwe, ndi dziko lidaungika ndi madzi ndi mwa madzi, pa mau a Mulungu;

6 mwa izi dziko lapansi la masiku aja, pomizika ndi madzi, lidaonongeka;

7 koma miyamba ndi dziko lamasiku ano, ndi mau omwewo zaikika kumoto, zosungika kufikira tsiku la ciweruzo ndi cionongeko ca anthu osapembedza.

8 Koma ici cimodzi musaiwale, okondedwa inu, kuti tsiku limodzi likhala kwa Ambuye ngati zaka cikwi, ndi zaka cikwi ngati tsiku limodzi.

9 Ambuye sazengereza nalo lonjezano, monga ena aciyesa cizengerezo; komatu aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena aonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.

10 Koma tsiku la Ambuye lidzadza ngati mbala; m'mene miyamba idzapita ndi cibumo cacikuru, ndi zam'mwamba zidzakanganuka ndi kurentha kwakukuru, ndipo dziko ndi nchito ziri momwemo zidzarenthedwa.

11 Popezaizi zonse zidzakanganuka kotero, muyenera inu kukhala anthu otani nanga, m'mayendedwe opatulika ndi m'cipembedzo,

12 akuyembekezera ndi kufulumira kwa kudza kwace kwa tsiku la Mulungu, m'menemo miyamba potentha mota idzakanganuka, ndi zam'mwamba zidzasungunuka ndi kutentha kwakukuru.

13 Koma monga mwa lonjezano lace tiyembekezera miyamba yatsopano, ndi ziko latsopano m'menemo mukhalitsa cilungamo.

14 Momwemo, okondedwa, popeza muyembekeza izi, citani cangu kuti mupezedwe ndi iye mumtendere, opanda banga ndi opanda cirema.

15 Ndipo yesani kulekerera kwa Ambuye wathu cipulumutso; monganso mbale wathu wokondedwa Paulo, monga mwa nzeru zopatsidwa cwa iye, anakulemberani;

16 monganso m'akalata ace onse pokanba momwemo za izi; m'menemo nuli zina zobvuta kuzizindikira, zinene anthu osaphunzira ndi osachazikika apotoza, monganso atero lao malembo ena, ndi kudziononga lao eni.

17 Inu, tsono, okondedwa, oozizindikiratu izi, cenjerani, kuti ootengedwa ndi kulakwa kwa iwo osayeruzika, mungagwe kusiya cichazikiko canu.

18 Koma kulani n'cisomo ndi cizindikiritso ca Ambure wathu ndi Mpulumutsi Yesu vistu; kwa iye kukhale uleme'ero, tsopano ndi nthawi zonse. Amen.

Mitu

1 2 3