2 Petro 1 BL92

1 SIMONI Petro, kapolo ndi mtumwi wa Yesu Kristu kwa iwo amene adalandira cikhulupiriro ca mtengo wace womwewo ndi ife, m'cilungamo ca Mulungu wathu ndi Mpulumutsi Yesu Kristu:

2 Cisomo kwa inu ndi mtendere zicurukitsidwe m'cidziwitso ca Mulungu ndi Yesu Ambuye wathu.

Atsate zokoma za Cikristu

3 Popeza mphamvu ya umulungu wace idatipatsa ife zonse za pamoyo ndi cipembedzo, mwa cidziwitso ca iye amene adatiitana ife ndi ulemerero ndi ukoma wace wa iye yekha;

4 mwa izi adatipatsa malonjezano a mtengo wace ndi akuru ndithu; kuti mwa izi mukakhale oyanjana nao umulungu wace, mutapulumuka ku cibvundi ciri pa dziko lapansi m'cilakolako.

5 Ndipo mwa ici comwe, pakutengeraponso cangu conse, muonjezerapo ukoma pa cikhulupiriro canu, ndi paukoma cizindikiritso; ndi pacizindikiritso codziletsa;

6 ndi pacodziletsa cipiriro;

7 ndi pacipiriro zipembedzo; ndi pactpembedzo cikondi ca pa abale; ndi pacikondi ca pa abale cikondi.

8 Pakuti izi zikakhala ndi inu, ndipo zikacuruka, zidzacita kuti musakhale aulesi kapena opanda zipatso pa cizindikiritso ca Ambuye wathu Yesu Kristu.

9 Pakuti iye wakusowa izi ali wakhungu, wa cimbuuzi, woiwala matsukidwe ace potaya zoipa zace zakale,

10 Momwemo abale, onjezani kucita cangu kukhazikitsa maitanidwe ndi masankhulidwe anu; pakuti mukacita izi, simudzakhumudwa nthawi zonse;

11 pakuti kotero kudzaonjezedwa kwa inu kolemerera khomo lakulowa ufumu wosatha wa Ambuye wathu ndi Mpulumutsi Yesu Kristu.

12 Mwa ici sindidzaleka kukukumbutsani inu nthawi zonse za izi, mungakhale muzidziwa nimukhazikika m'coonadi ciri ndi inu.

13 Ndipo ndiciyesa cokoma, pokhala ine m'msasa uwu, kukutsitsimutsani ndi kukukumbutsani;

14 podziwa kuti kuleka kwa msasa wanga kuli pafupi, monganso Ambuye wathu Yesu Kristu anandilangiza.

15 Koma ndidzacitanso cangu kosalekeza kuti nditacoka ine, mudzakhoza kukumbukila izi,

16 Pakuti sitinatsata miyambi yacabe, pamene tinakudziwitsani mphamvu ndi maonekedwe a Ambuye wathu Yesu Kristu, koma tinapenya m'maso ukulu wace.

17 Pakuti analandira kwa Mulungu Atate ulemu ndi ulemerero, pakumdzera iye mao otere ocokera ku ulemerero waukuru, Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa, amene Ine ndikondwera naye;

18 ndipo mau awa ocokera Kumwamba tidawamva ife, pokhala pamodzi ndi iye m'phiri lopatulika lija,

19 Ndipo tiri nao mau a cinenero okhazikika koposa; amene mucita bwino powasamalira, monga nyali younikira m'malo a mdima, kufikira kukaca, nikauka nthanda pa mtima yanu;

20 ndi kudziwa ici poyamba, kuti palibe cinenero ca lembo citanthauzidwa pa cokha,

21 pakuti kale lonse cinenero sicinadza ndi cifuniro ca munthu; koma anthu a Mulungu, ogwidwa ndi Mzimu Woyera, analankhula.

Mitu

1 2 3